Encyclopaedic Compendia |
Hullquist Central |
Ecclectic Interchange |
Mutu 12
Nkhani yaikulu inali pafupi. Satana ananena kuti dziko lapansi ndi lake ndipo anazitcha yekha "mfumu ya dziko lino." Anaonetsera kuti anthu adamsankha iye monga wolamulira wawo. Kupyolera mwa wanthu analamulira dziko. Khristu anabwera kudzatsutsa zolankhula za Satana. Monga mwana wa munthu, Khristu anaima njii kwa Mulungu. Pamenepo zinaonekera kuti Satana sanalande kotheratu pfuko la wanthu, ndikutinso kubetchera kwake kudziko kunakhala kwa bodza. Onse amene anafuna kuomboledwa ndi mphamvu yake adzamasulidwa. Satana anadziwa kuti sanali ndi ulamuliro wonse pa dziko, munaoneka mwa wanthu mphamvu zimene zinayima kuulamuliro wake. Mu zinsembe zopelekedwa ndi Adamu ndi ana wake anazindikira kuti inali njira ya chigwirizano pakati pa dziko lapansi ndi la kumwamba. Satana anaganiza mwa iye yekha kuti asokoneze chigwirizanochi. Anamunenera Mulungu zoipa ndi kumasulira uyo njira zimene zinkalozera kwa Mpulumutsi. Anthu anatsogozedwa kuopa Mulungu monga Iye amene ankakondwera ndi chionongeko chawo. Zinsembe zimene zikanabvumbulutsa chikondi chake zinapereka kuti ziitane mkwiyo wake. Onani Genesis 3;15. Pamene mawu a Mulungu anaperekedwa m'malembo Satana anayamba kuwerenga maulosi. Kuchokera m'badwom'badwo anagwira ntchito yakuphimba wanthu m'maso kuti amkane Khristu pakubwera kwake. Pakubadwa kwa Yesu, Satana anadziwa kuti wina wabwera kudzakangana ndi ulamuliro wake. Kuti mwana wa Mulungu abwere ku dziko lapansi monga munthu wodzazidwa ndi uyamiko. Moyo wodzikonda wa Satana sunathe kumuonetsera chikondi ichi. Kuyambira pamene anagwa kumwamba wakhala akupangitsa anthu kugawana nawo kugwa kwake. Ankawapangitsa anthu kuchepetsa zinthu za kumwamba, ndikuika mtima pa zinthu za m'dziko. Satana Atsimikiza Kugonjetsa Pa ubatizo wa Mpulumutsi, Satana anamva liu la Yehova kudziwitsa umulungu wa Yesu. Tsopano Yesu anabwera "m'chifanizo cha thupi la uchimo" (Aroma 8:3), Atate mwini wake analankhula. Analumikizana ndi wanthu m'mbuyomo kupyolera mwa Khristu; tsopanonso alumikizana ndi wanthu mwa Khristu yemweyo. Tsopano zinaonekeratu kuti chigwirizano pakati pa munthu ndi Mulungu chinabwereranso. Satana anaona kuti ayenera kugonjetsa kapena kugonja. Mphamvu zonse za mpatuko zinalimbana ndi Khristu. Ambiri anaona mkangano pakati pa Khristu ndi Satana ngati wopanda phindu pa miyoyo yawo. Koma mumtima wa munthu aliyense mumakhuzidwa. Zinyengo zimene Khristu anapewa ndi izo zimene timapeza zobvuta kuima nazo. Ndi kulemera kwa machimo a m'dziko pa Iye, Khristu anagonjetsa yeso pa chilakolako, pa chikondi cha dziko, ndi pa chikondi cha kudzionetsera chimene chimatsogolera kuchikayiko. Awa ndi mayeso amene anagonjetsa Adamu ndi Hava, ndi amenenso mosapeneka amatigonjetsa ife. Satana analoza pa uchimo wa Adamu monga chotsimikizira kuti malamulo a Mulungu sangasungike. Mu umunthu wathu, Khristu anadza kuwombola kulephera kwa Adamu. Koma pamene Adamu anatsatidwa ndi woyesayo, zotsatira za uchimo sanazidziwe. Anaima ndi mphamvu zonse za umuna, ndikukhala nawo maganizo a mphamvu ndi thupi. Atazunguliridwa ndi ulemerero wa Edeni, nthawi zonse anali kucheza ndi anthu akumwamba. Sizinali choncho pamene Khristu analowa m'chipululu kukakomana ndi Satana. Kwa zaka zikwi zinayi mtundu unakhala ukuchepa mphamvu za m'thupi, m'maganizo, ndi m'khalidwe; ndipo Khristu anatenga pa iye nkhawa za umunthu wochepetsedwayo. Ndi pokhapo akanaombala munthu kuchokera pansi penipeni pa kugwa kwake. Ananyamula Nkhawa Zonse za Umunthu Ichi chinasonyeza kusakhulupirira. Ngati Yesu akanachita chimene Satana ankafuna, akanabvomereza kukaika kwake. Satana anafuna kuika ganizo mwa Hava la kuti kukaniza chipatso chokongola sichinali kutsutsana ndi chikondi cha Mulungu pa munthu. Choncho tsopano oyesayo anafuna kuuzilira Khristu zokhumba zake. "Ngati uli Mwana wa Mulungu." Mu mawu ake anaonetsera kudabwa. Kodi Mulungu angazunze mwana wake chonchi, ndikumusiya iye m'chipululu ndi zirombo za m'nkhalango, opanda chakudya, chisoni, ndi m'pumulo? Iye anasonyeza kuti Mulungu sanatanthauze kuti Mwana wake adzakhala m'mazunzo otere. "Ngati uli mwana wa Mulungu," onetsa mphamvu Yako. Lamulira kuti mwalawu ukhale mkate. Chikaiko M'ku Yesedwa Satana anachita ukatswiri wake wonse. Iye anati, mmodzi wa angelo a mphamvu wagwetsedwa kuchokera kumwamba. Ndipo nkhope ya Yesu inaoneka ngati kuti ogwetsedwayo anali Iye, okanidwa ndi Mulungu ndi anthu omwe. Umulungu ukadaonekera pakuchita chozizwa: "ngati uli Mwana wa Mulungu, lamula mwalawu kukhala mkate." Ndimchitidwe wa mphamvu ya kulenga poumirizidwa ndi Satana chinakakhala chitsimikizo chotsiriza cha umulungu. Ndipo kukangana kwao kudakatheratu nthawi yomweyo. Koma Iye sadafune kumuonetsera Satana umulungu wake. Zikadakhala kuti Khristu anagwirizana nazo zonena za mdaniyo, Iye akadatibe undionetse chizindikiro kuti ndiwe mwana wa Mulungu. Ndipo kunali kosatheka kuti Khristu awonetsere mphamvu ya Umulungu mwa Iye yekha. Iye anadza kudzayesedwa monga ife, ndikutisiyira chitsanzo. Ntchito zake zodabwitsa zinali zaphindu kwa onse. Molimbikitsidwa polingalira mawu ochokera kumwamba, Yesu anatsamira m'chikondi cha Atate wake. Yesu anagonjetsa Satana ndi malemba. Nati, "Kwalembedwa." Chida chake cha nkhondo chinali mawu a Mulungu. Satana anafunitsitsa chozizwa cha Khristu. Koma chomwe chinali choposa zozizwa zonse, ndiko kudalira kwathunthu pa mawu oti "pakuti Ambuye wanena," ichi chinali chizindikiro chothetsa mkangano. Ndipo Yesu pogwiritsitsa udindo wake oyesayo anasowa chochita. Mu nthawi zomwe kufooka kunakula Khristu anakomana ndi mayesero akulu kwambiri. Apa ndi pomwe Satana anapezerapo mwayi wa kufooka kwa umunthu. Pamene wina agwetsedwa mphwayi ndi usauki, Satana amakhala ali chete ku muyesa iye pogonjetsa mbali zofooka za khalidwe kuti agwedeze kudalira kwathu mwa Mulungu. Kawirikawiri Satana amabwera monga momwe anamufikira Khristu nadzikonzetsera pamaso pa kufooka kwathu. Iye amayembekezera kukhumudwitsa moyo ndi kuswa chigwirizano chathu ndi Mulungu. Koma ngati timfikira iye monga Yesu anachitira, tidzatha kuzemba chigonjetso chake. Onani Numeri 20:1-13; Mafumu woyamba 19:1-14. Yesu anati kwa woyesayo, "munthu sangakhale ndi moyo ndi mkate wokha koma ndi mawu ochokera mkamwa mwa Mulungu." Pasanapite zaka zoposa mazana khumi ndi mphamvu zinayi m'chipululu, Mulungu anali kuwadyetsa anthu ake ndi mana wochokera kumwamba. Ichi chinali kuwaphunzitsa iwo kuti pamene a khulupirira mwa Mulungu ndi kuyenda m'njira zake sadzatayidwa konse. Kupyolera m'mawu a Mulungu zakudya zinkaperekedwa kwa a Heberi, ndipo m'mawu omwewo chidaperekedwanso kwa Yesu. Iye anayembekezera kuti Mulungu amudyetse. Sakadatha kupeza chakudya pongotsata zomwe Satana ankafuna. Kunali kwabwino po kubvutika ku chilichonse chakudya koposa kulekana ndi chifuniro cha Mulungu. Kawirikawiri wotsatira a Yesu amaperekedwa komwe chifuniro cha Mulungu chilimbana ndi chifuniro cha munthu. Satana angampange iye kuti aperekedi chikumbumtima chachikhulupiriro chake. Koma chinthu chimodzi chomwe tingachidalire ndi mawu a Mulungu. Pamene ife tiphunzira za mphamvu ya mawu ake, sitidzatha kutsata zokhumba za Satana m'malo moti tipeze chakudya pena chipulumutso cha miyoyo yathu. Tidzamvera lamulo la Mulungu ndikukhulupirira lonjezano Lake. Mateyu 6:33. M'kukangana kwakukulu komaliza ndi Satana okhulupirira Mulungu adzaona zonse zothandizira dzikoli zitalekana. Ndi kamba koti sadzalola kuswa lamulo lake, iwo sadzalowedwa kugula ngakhale kugulitsa. Koma kwa omvera, lonjezano laperekedwa; "adzakhala kumwamba ndipo mkate wake udzapatsidwa kwa iye ndi madzi ake oyera." Pamene m'dziko mungagwe njala, iwo adzadyetsedwa. Onani Chibvumbulutso 13:17. Yesaya 33:16. Masalimo 37:19. Kusadziletsa Kugwetsa Ubwino Khristu anati kuti kubwera kwake kwa chiwiri kusanayandikire dziko lidzakhala chimodzimodzi monga m'masiku a Nowa chigumula chisanafike ndi monganso zinalili mu Sodomu ndi Gomora. Kwa ife zikhale monga phunziro la kufulumizitsa Mpulumutso. Pakupyolera m'kuwawidwa kosaneneka kwa Khristu tingathe kuona kuipa kwa tchimo. Chiyembekezo chathu chokha cha moyo wosatha chili pakupereka zokhumba zathu ndi zisoni ku chifuniro cha Mulungu. Mwa ife tokha ndikosatheka kukana kugwa kwa umunthu wathu. Koma m'masiku a moyo wathu Mbuye watikonzetsera njira yakuti tigonjetse. Iye sadzatilola kudzadzidwa mphayi ndi mantha. Yesu anati, "Limbikani mtima," "ndaligonjetsa dziko lapansi." Yohane 16:33. Iye wakulimbana ndi mphamvu za zilakolako zake ayang'ane Mpulumutsi kumayesero m'mchipululu. Muoneni Iye kusautsidwa kwake pa mtanda alikunena, "ndili ndi ludzu." Mphotho Yake ndi yathu. Yesu anati, "karonga wa dziko lino wabwera, ndipo alibe nane kanthu." Ndipo mwa Iye panalibe chomwe chinagwirizana ndi maganizo a Satana. Iye sanachimwe. Ngakhale m'maganizo omwe sanayesedwe. Choncho zingakhale chimodzimodzi ndi ife. Umunthu wa Khristu unagwirizana ndi umulungu; Iye anayeneradi kulimbana ndi mzimu woyera wokhazikikawo. Ndipo Iye anadza kutipanga ife kuti titengere umulungu wake. Mulungu amafikira dzanja la chikhulupiriro mwa ife kulitsogolera kugwiritsitsa umulungu wa Khristu, kuti tikhale mu ungwiro wa khalidwe Lake. Johane 14:30. Momwe izi zinachitikira, Khristu wationetsera. Kodi Khristu anamugonjetsa Satana mwa njira yanji? Ndi mawu a Mulungu. Iye anati, "Kwalembedwa." Ndipo lonjezano lililonse m'mawu a Mulungu ndi lathu. Pamene tili m'mayesero tiyenera kuyang'ana Mphamvu ya Mawu. Ndipo mphamvu zake zonse ndi zathu. Onani 2 Petro 1:4. Masalmo 119:11; 17:4.
|