Mutu 1 |
Chichewa | Mutu 2 |
K UCHOKERA MASIKU OSAYAMBA, Ambuye Yesu Khristu anali pamodzi ndi Atate; Iye anali “fanizo la Mulungu,” ndi “chinyezimiro cha ulemerero wake.” Yesu anabwera ku dzikoli lodetsedwa ndi uchimo kudzasonyeza kuŵala kwa chikondi cha Mulungu. Chotero ananenera za Iye, “Adzatchedwa dzina lake Emanuele…Mulungu ali nafe.” Akolose 1:15; Ahebri 1:3; Isaiya 7:14; Mateyu 1:23. Yesu Khristu anali Mawu a Mulungu—ganizo la Mulungu lomveka bwino. Chibvumbulutsochi sichinaperekedwa kwa ana Ake okha amene anabadwa padziko lino lapansi ayi, koma kwa munthu aliyense. Dziko lathu laling'ono ndi buku la maphunziro la chilengedwe chonse. Wonse woomboledwa ndi wosachimwa adzapeza mu mtanda wa Khristu phunziro ndi nyimbo zawo. Adzaona kuti ulemerero wa kuŵala pankhope pa Yesu uli ulemerero wa chikondi cha nsembe yodzipereka. Adzaona kuti lamulo la moyo wa dziko lapansi ndi Kumwamba lili lamulo lachikondi chopanda dyera. Chikondi chimene “sichitsata za mwini yekha”, chili chopezedwa mumtima wa Mulungu ndi m'moyo wa Yesu amene ali “Wofatsa ndi Wodzichepetsa mtima,” 1Akorinto 13:5; Mateyu 11:29. Poyamba, Khristu yekha anaika maziko a dziko lapansi. Dzanja Lake linapachika maiyko a m'mwamba m'miyamba napanga maluŵa a m’munda. Iye anadzaza dziko lapansi ndi kukoma, ndi nyimbo m'mlengalenga. Pa zinthu zonse za padziko lapansi, ndi thambo, ndi kumwamba, Iye analemba uthenga wachikondi cha Atate. Masalmo 65:6; 95:5. Tsopano tchimo laononga ntchito yangwiro ya Mulungu, koma malemba achikondiwo alipobe. Kulibe kanthu kalikonse kamene kamakhala pa kokha koma mtima wadyera wa munthu. Palibe mbalame ya m'mlengalenga, kapena nyama ya padziko, kapena udzu wochepetsetsa, zimene sizimatumikira anthu ndi nyama. Ndipo anthu ndi nyama zimatumikiranso miyoyo ya mtengo, duŵa, ndi tsamba. Dzuŵa limaŵalitsira kuunika kwake kusangalatsa mayiko ambirimbiri. Nyanja imalandira mitsinje ku dziko koma imalandira ndi cholinga cha kupatsanso. Angelo mu ulemerero amalandira chimwemwe chawo pakupereka. Amabwera ku dzikoli lodetsedwa ndi kuunika kuchokera mabwalo a Kumwamba kuŵasonkanitsa wosokera ku chiyanjano ndi Khristu. Koma kuona Mulungu kwenikweni tiziyang'ana kwa Yesu. Tizindikira kuti ulemerero wa Mulungu uli kupatsa. Khristu anati, “Ine sinditsata ulemerero wanga,” “koma ulemu wa Iye amene anandituma.” Khristu analandira zinthu zonse kwa Mulungu, koma Iye analandira ndi cholinga cha kupatsa. Mwa Mwana, moyo wa Atate umayenda kutumphukira kwa zolengedwa zonse; mwa Mwana umabwerera ndi utumiki wachimwemwe monga mtsinje wachikondi kwa Wopatsa wamkulu. Chotero mwa Khristu kukoma mtima kuli kwamphumphu. Yohane 8:50; 7:18. Kumwamba Lamuloli Linaswedwa U CHIMO UNAYAMBA ndi kudzikuza. Lusifala, kerubi wakuphimba, anafuna kukhala woyamba Kumwamba. Anayesa kukoka anthu a kumwamba ku ŵachotsa kwa Mlengi wawo, ndi kudzilandirira yekha chipembedzo chawo. Pakuyesa kumubveka Mlengi wokonda ndi makhalidwe ake oipa, anatsogolera angelo kupeneka mawu a Mulungu ndi kusakhulupirira kukoma mtima Kwake. Satana anaŵapangitsa iwo kuyang’ana Iye ngati Woopsya wosakhululukira. Chotero ananyenga angelo. Chotero ananyenga anthu, ndipo usiku wa tsoka unagwa padziko lapansi. Dziko lapansi linali mu mdima ndi kusazindikira za Mulungu. Ndipo chifukwa layenera kubwezeredwa kwa Mulungu, mphamvu yonyenga ya Satana inayenera kuthyoledwa. Koma chimenechi sichiyenere kupangidwa ndi mphamvu yokakamiza. Ntchito ya mphamvu itsutsana ndi maziko a boma la Mulungu; Iye afuna utumiki wa chikondi chokha; ndipo chikondi sichingathe kulamulidwa ndi mphamvu. Chikondi chingathe kutsitsimutsidwa ndi chikondi chokha. Kudziŵa Mulungu ndi kumukonda Iye. Makhalidwe Ake ayenera kuyerekezedwa ndi makalidwe a Satana. Mmodzi yekha m'maiko onse angathe kuchita ntchitoyi. Iye yekha amene anadziŵa kuya ndi utali wa chikondi cha Mulungu, ndiye angathe kuchionetsera. Nzeru ya chiombolo yathu siinapangidwe atagwa Adamu. Inali chibvumbulutso cha “chinsinsi chimene chinabisika mwa nthaŵi zonse zosayamba.” Kunali kumasula kwa chikonjetsero cha nthaŵi zosayamba cha maziko a ufumu wa Mulungu. Mulungu ndi Khristu anadziŵiratu kuti uchimo udzaloŵa. Mulungu sanalamulire kuti zoipa zidzakhale, koma anaikiratu njira yogonjetsera ngozi yoopsyayi. Chikondi chake padziko lapansi chinali chachikulu chotero kuti anapangana kupatsa “Mwana wake wobadwa yekha kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Aroma 16:25; Yohane 3:16. Lusifala anati, “Ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;…ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.” Koma Khristu, “pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu.” Yesaya 14:13,14; Afilipi 2:6,7. Nsembe Yaulere NSEMBE IMENEYI inali yaulere. Yesu akadasunga ulemerero wa kumwamba ndi chilemekezo cha angelo. Koma anasankha kudzitsitsa kuchokera pa mpando wa ufumu wa chilengedwe chonse, kuti akhoze kubweretsa moyo kwa otaika. Pafupi zaka zikwi ziwiri zapitazo, mawu anamveka mumwamba. “Thupi munandikonzera Ine.” Khristu anali pafupi kubwera ku dziko lathu lino kudzabadwa monga munthu. Ngati akanabwera ndi ulemerero Wake umene anali nawo dziko lisadapangidwe, sitikadatha kupirira kuŵala kwa pankhope. Kuti tithe kumuona Iye osaonongedwa, ulemerero Wake unaphimbidwa. Umulungu Wake unaphimbidwa ndi umunthu. Ahebri 10:5. Nzeru iyi yaikulu inasonyezedwa ndi zizindikiro ndi zionetsero. Chilangali chamoto, chimene Khristu anamuonokera Mose, chinaonetsera Mulungu. Mulungu Wosatha anadzibvundikira m’chitsamba wamba kuti Mose akadachiyang'ana nakhala ndi moyo. Ndi m’mtambo usana ndiponso mtambo wamoto usiku, ulemerero wa Mulungu unali wophimbidwa kuti anthu akadatha kuona. Chotero Khristu anali kudza mu “thupi lathu lopepulidwa”, “mu mafanizidwe a anthu.” M’maso a dziko lapansi Iye sanali okongola kuti timfune; koma Iye anali Mulungu wobadwa m’thupi. Ukulu Wake unali kubisidwa kuti akanayandikira pafupi ndi anthu obvutika. Afilipi 3:21. Mulungu analamulira Mose, “Andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pawo.” Poyendayenda m’chipululu, chizindikiro cha kukhala kwake, mkachisi, chinali nawo. Chotero Khristu anaimitsa hema Wake pambali pa mahema a ŵanthu, kuti tizoloŵerane ndi khalidwe Lake la Umulungu. “Ndipo Mawu anasanduka thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero Wake…wodzala ndi chisomo ndi choonadi.” Eksodo 25:8; Yohane 1:14. Satana amaonetsera ngati kuti lamulo la Mulungu la chikondi ndi lamulo la kudzikonda wekha. Amanena kuti lili losatheka kuti tingalimvere. Kugwa kwawo kwa makolo anthu oyamba pamodzi ndi tsoka lililonse, iye akuyimba mlandu Mlengi, kuŵatsogolera anthu kuyang'ana Mulungu ngati Mlengi wa tchimo ndi kubvutika ndi imfa. Yesu analiika poyera bodza limeneli. Monga munthu nzathu, Yesu anationetsa chitsanzo cha kumvera. Potero anabvala makhalidwe athu ndipo anapyola m’machitidwe athu. “Mu zinthu zonse kudamuyenera kufanizidwa ndi abale.” Ngati ife tiyenera kupirira kanthu kena kamene Yesu sanapirire, pomwepo Satana akadaganiza kuti mphamvu ya Mulungu ili yochepa ndipo ndi yosakwana kutiombola. Kotero Yesu “anayesedwa m’zonse monga ife.” Iye anapirira mayeso onse amene tingapeze. Komabe sanagwiritse ntchito mphamvu iliyonse yopitirira imene anatipatsa ife. Monga munthu, anakumana nawo mayeso ndipo anagonjetsa uchimo ndi mphamvu imene Mulungu anampatsa. Anaonetsera bwino khalidwe la lamulo la Mulungu. Moyo Wake umachita umboni kuti ife tingamverenso lamulo la Mulungu. Aheberi 2:17; 4:15. Ndi umunthu Wake, Khristu anakhudza anthu; ndi umulungu Wake wagwira mphando wa chifumu wa Mulungu. Monga Mwana wa munthu anatipatsa chitsanzo cha kumvera, monga Mwana wa Mulungu, akutipatsa mphamvu ya kumvera. Anatiuza, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine kumwamba ndi pa dziko lapansi.” Khristu nafe ndiye chitsimikizo cha chiombolo chathu kuchoka kutchimo, chitsimikizo cha mphamvu Yake yotithangata kumvera lamulo la kumwamba. Mateyu 28:18. Khristu anatisonyeza makhalidwe osiyana ndi Satana. “Popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.” Khristu anatenga maonekedwe a kapolo, napereka nsembe, Iye yemwe nakhala nkulu wansembe ndipo Iye yemwe nakhala nsembe imene. “Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu.” Yesaya 53:5; Afilipi 2:8. Iye Anazunzidwa YESU KHRISTU anazunzidwa monga ife tiyenera kuzunzidwa, kuti ife tidzakhale mu ulemerero Wake. Ana ŵeruzidwa chifukwa cha zolakwa zathu zimene analibe gawo, kuti tikayesedwe wolungama ndi chilungamo Chake chimene tinalibe gawo. Anazunzika ndi imfa yathu, kuti ife tikalandire moyo Wake. “Natundunzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu...ndipo ndi mabala Ake ife tachiritsidwa.” Yesaya 53:5. Chifuniro cha Satana chinali cha kulekanitsa munthu ndi Mulungu pakati pake kwa muyaya, koma pakutenga maonekedwe athu, Mpulumutsi anadzilumikiza ndi umunthu ndi mfundo zosaduka. “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana Wake wobadwa yekha.” Sanangom’pereka kudzangokhala nsembe yathu, koma anam’pereka kukhala mmodzi wa banja la anthu, kunyamula makhalidwe athu a umunthu ku nthaŵi yamuyaya. Yohane 3:16. “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lache.” Mulungu anatilandira umunthu mwa mwana Wake, ndipo adakauloŵetsa kumwamba kwa Mulungu. “Mwana wa munthu” adzamutcha dzina Lake “Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.” Amene ali “woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa,” alibe manyazi kutitcha ife abale. Kumwamba kukulumikizidwa bwino m’umunthu, ndi umunthu ukufungatiridwa m'chifuwa cha chikondi chosatha. Yesaya 9:6; Ahebri 7:26; 2:11. Kukwezeka kwa woomboledwa kudzakhala umboni wosatha wa chisomo cha Mulungu. Adzaonetsera “m’nyengo zili nkudza chuma choposa cha chisomo chake, m’kukoma mtima kwake pa ife mwa Khristu Yesu” kuti “nzeru ya yaikulu ya Mulungu” ikazindikiritsidwe kwa “akulu ndi maulamuliro m’zakumwamba.” Aefeso 2:7; 3:10. Kupyolera mu ntchito ya Khristu, ufumu wa Mulungu umaoneka wolungama. Iye Wamphamvuyonse ali kudziŵidwa ngati Mulungu wa chikondi. Mlandu wa Satana uli kugonjetsedwa, ndi makhalidwe ake ali kuululidwa. Uchimo sungathe kuloŵanso M’mayiko onse. Mayikowa sadzaloŵanso mumpatuko kwa nthaŵi zonse. Chifukwa cha nsembe yodzipereka ya chikondi, dziko lapansi ndi kumwamba zamangiriridwa kwa Mlengi ndi mfundo imene siingathe kuduka. Pamene uchimo umachuluka, pomwepo chisomo cha Mulungu chimachuluka koposa. Dziko lapansi, pamene Satana amati ndi lake, lidzalandira ulemu woposa mayiko ena onse. Kuno, kumene Mfumu yaulemerero inakhala niibvutika ndipo niifa—kuno nkumene chihema cha Mulungu chidzakhala mwa anthu, “ndi Mulungu yekha adakhala nawo, nadzakhala Mulungu wawo.” Kwa nthaŵi yosatha woomboledwa adzamlemekeza chifukwa cha mphatso Yake yosaneneka—Emanuele, ‘Mulungu ali nafe.’ Chibvumbulutso 21:3. |
Chichewa | Mutu 2 |