HOME
Mutu 1Mutu 2 Mutu 3
Anthu Wosankha

K WA ZAKA ZOPOSERA CHIKWI CHIMODZI Ayuda anali kudikira kubwera kwa Mpulumlutsi. Koma pakudza pake sanamudziŵe Iye. Sanaone mwa Iye ubwino uli wonse kuti angamukhumbe.  “Anadza kwa ake a Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamulandira Iye.” Yesaya 53:2; Yohane 1:11.
      Pakati pa mitundu yonse Mulungu anasankha Aisraeli kusunga zizindikiro ndi uneneri zimene zinakaonetsera Mpulumutsi.  Anaŵasankha kuti akhale ngati zitsime za chipulumutso kudziko lapansi. Mtundu wa Aheberi unayenera kusonyezera Mulungu pakati pa amitundu. Pakuitanidwa kwa Abrahamu, Ambuye anati, “Mwa iwe mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.” Ambuye ananena kupyolera mwa Yesaya, “Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopempherera anthu onse.” Genesesi 12:3; Yesaya 56:7.
      Koma Aisraeli anaika ziyembekezo zawo pa za dziko ndipo anatsatira njira za akunja. Mulungu anaŵatumizira chenjezo kupyolera mwa aneneri Ake koma sizinatanthauze kanthu. Popanda chifukwa iwo anabvutitsidwa ndi anthu akunja. Kukonzanso kuli konse kunatsatiridwa ndi chimpatuko chachikulu choposa.
      Ngati Aisraeli akanakhala woona kwa Mulungu, akanaŵapanga iwo “koposa amitundu onse anaŵalenga, wolemekezeka, womveka ndi waulemu.” “Mitundu ya anthu yomwe idzamva malemba onse aŵa,” adzanena “Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.” Deuteronomo 26:19; 4:6.
      Koma chifukwa kukhulupirira kwawo, chifuniro cha Mulungu chidakwanitsidwa kupyolera mumikangano ndi zunzo. Anatengedwa kupita ku Babuloni ndi kumwazidwa maiko a anthu akunja. Pamene anali kulirira chifukwa cha kachisi woyera amene anawonongedwa, kupyolera mwa iwo nthano ya Mulungu inafalitsidwa pakati pa amitundu. Maperekedwe ansembe za achikunja zinali chisokonezo cha maperekedwe ansembe omwe anaŵakhazikitsa Mulungu. Ambiri anaphunzira kupyolera mwa Aheberi tanthauzo la utumiki woyerawu ndipo nchikhulupiriro anagwira lonjezo la Mombolo.
      Siapang'ono okha amene anataya miyoyo yawo chifukwa chokana kusunga Sabata ndi kumvera zipembedzo zachikunja. Pamene opembedza mafano anatsimikiza kuphwanya choonadi, Ambuye anatumiza anchito Ake pamaso pa mafumu ndi olamulira kuti iwo ndi anthu awo alandire kuŵala. Mafumu aakulu anatsogoleredwa kuti anenere ukulu wa Mulungu yemwe akapolo awo Aheberi anamulambira.
      Mzaka zikwi zingapo atangochokera ku ukapolo wa ku Babuloni, Aisraeli anachiritsidwa kuzipembedzo za milungu yachikunja, ndipo anatsimikiza kuti chipambano chawo chinakhazikika pakumvera malamulo a Mulungu. Koma anthu ambiri maganizo awo anali adyera. Mapembedzedwe awo anali kufuna kuonetsera ukulu wawo ndi kudziŵika kwawo monga mtundu. Sanakhale kuunika kwa dziko lapansi, koma anadzibisa okha kuopa mayesero. Mulungu anapereka malamulo pa iwo ndi cholinga choti asalumikizane ndi amafano kuti angalowerere m'njira zachikunja. Koma langizoli sanalimasulire bwino. Linagwiritsidwa ntchito ngati chinga pakati pa ana Aisraeli ndi mitundu ina. Ayuda anali ansanje ndi akunja poganiza kuti Mulungu angaonetsere iwo chisomo!

M'mene Anasokonezera Machitidwe a Mapemphero
A TABWERERA KUCHOKERA KU BABULONI,  matchalitchi ang'ono anamangidwa mudziko lonse, kumene malamulo anaphunzitsidwa ndi ansembe ndi alembi. Masukulu ambiri anali kunenera kuti amaphunzitsa ndondomeko za chiyero. Koma nthaŵi ya ukapolo anthu ambiri analandira ziphunzitso zachikunja, ndipo izi anazitengera iwo m'mapemphero awo. Za miyambo yamaperekedwe ansembe anaika ndi Khristu mwini. Ichi chinali chizindikiro cha Iye, odzazidwa ndi thanzi ndi kukongola. Koma Ayuda anataya moyo wa uzimu m'malalikidwe awo ndipo anakhulupirira za nsembe ndi malamulo awo m'malo mwa Iye amene zimalozera. Ansembe ndi aphunzitsi anapanga zifuniro zawo zambiri kuti akwaniritse zimene zina ŵasoŵa; ndipo pakuchuluka kwa zifuniro zawo chikondi cha Mulungu chinazilala mwa iwo.
          Iwo amene anayesa kusunga malamulo ochepa aaphunzitsi sanapeze mpumulo mchikumbumtima chawo. Motero Satana anagwira ntchito yoŵakhumudwitsa anthu, kuwononga ganizo lawo la makhalidwe a Mulungu ndi kupanga chikhulupiriro cha Aisraeli kuti chikhale chonyozeka. Anafuna kutsimikiza ganizo lake loti malamulo a Mulungu ndi wokhwima kotero kuti munthu sangathe kuwasunga. Angakhale Aisraeli, iye ananena kuti, sanasunge lamulo.

Kuyembekeza Mpulumutsi Onama
A YUDA ANALIBE kudziŵa koona za ntchito ya Mpulumutsi. Sanafunitsitse kupulumutsidwa kuchokera ku tchimo, koma ku ukapolo wa Roma. Analakalaka kuti Mombolo adzaŵakweze Aisraeli kuti alamulire dziko lonse. Chotero njira yomukanira Mpulumutsi.
          Pobadwa pa Khristu, mtunduwo unali kudandaula ndi kulamulidwa ndi ambuye adziko lina, ndipo unali kusokonezedwa ndi ndewu yachiweniweni. Aroma ndiwo amene amasankha ndi kuchotsa mkulu wansembe, kotero kuti wena amachita kuperekera ziphuphu kapena kupha anzawo kuti iwo asankhidwe. Chotero unsembe unakhala wobvunda. Anthu amalamulidwa mwankhanza, ndipo Aroma amalipitsa nsonkho waukulu. Kusakwanitsidwa, dyera, mbanda, kusakhulupirirana, ndi kupeputsa zinthu za uzimu zinali kuwononga kwambiri mtima wake wamtundu wa Israeli.
          Mumdima wawo ndi m'kuponderezedwa kwawo, anthu analakalaka Munthu amene akanakonza ufumu wa Israeli. Iwo anaphunzira ulauli, koma opanda maso auzimu. Choncho anamasulira ulauli mwa zifuniro zawo za dyera.

Mutu 1 Mutu 3