Mutu 3 |
Mutu 2 | Mutu 4 |
P AMENE ADAMU ndi hava m’munda wa Edene, poyamba anamva lonjezo la kubwera kwa Mpulumutsi, anayembekeza kuti lidzakwanitsidwa msanga. Anamlandira mwana wawo wamwamuna woyamba ndi chisangalalo ndi chiyembekezo chakuti iye akadakhala Mombolo. Koma iwo amene analandira lonjezolo poyamba, anafa lisanakwaniritsidwe. Lonjezo linabwerezedwa kupyolera mwa makolo ndi aneneri kuŵathandiza kukumbukira chiyembekezo cha kubwera Kwake. Koma sanabwere. Ulosi wa Danieli unaulula nthaŵi ya kudza kwake, koma sionse amene anamasulira bwino uthengawu. Mbadwo ndi mbadwo unapitirira. Manja a oŵazinga ana a Israeli analimbikirabe; ndipo ambiri anakonzeka kupfuula, “Masiku achuluka, ndi masomphenya alionse apita pachabe.” Ezekieli 12:22. Koma monga nyenyezi zimatsata njira zawo, zifuniro za Mulungu zilibe kufulumira kapena kuchedwa. Uphungu waukulu wa Kumwamba unaikiratu nthaŵi ya kudza kwa Yesu Khristu. Ndipo pamene nthaŵiyo inakwana, Yesu anabadwa ku Betelehemu. “Pamene nthaŵi inakwana, Mulungu anatuma Mwana wake.” Dziko lapansi linali lokonzekera kubwera kwa Mombolo. Mitundu inali yogwirizana pansi pa boma limodzi. Panali chinenero chimodzi chimene anthu ambiri amalankhula. Ayuda amadera onse amene adabalalitsidwa ndi nkhondo anasonkhana ku Yerusalemu ku maphwando a pachaka. Pobwerera kwawo, akadafalitsa uthenga wobwera kwa Mesiya. Agalatiya 4:4. Nthaŵi ija njira zonse za Chikunja zinali kutaya chikoka chawo pa anthu. Anthu anafuna chipembedzo choti chikwaniritse mitima yawo. Miyoyo imene inali kusakasaka kuŵala inali ya ludzu yofuna kudziŵa choonadi cha Mulungu wa moyo, ndi kutsimikiza kwa moyo itapita imfa. Ambiri anafuna Mpulumutsi C HIKHULUPIRIRO CHA AYUDA chinazilala, ndipo chikhulupiriro cha zinthu za m’tsogolo chinayamba kuzilala. Kwa ambiri, imfa inali chisinsi choopsya; tsogolo lawo linali losatsimikizika ndi loopsya. “Muchigwa chamthunzi wa imfa” anthu anakhala opanda owasangalatsa. Ndi chidwi anayang’anira kubwera kwa Mpulumutsi, pamene chinsinsi cha m’tsogolo chiti chidzakhale pa m’mbalambanda. Kunja kwa mtundu wa Ayuda kunali anthu ofunafuna choonadi, ndipo kwa iwo Uzimu wa Chinenero unaŵadzera. Mawu awo a uneneri anayatsa chikhulupiriro m’mitima ya anthu zikwizikwi achikunja. M'zaka mazanamazana malemba akhala ali kumasuliridwa mu chinenero cha Chigiriki, chimene chinali chiyankhulo muufumu wonse wa Chiroma. Ayuda anamwazika ponseponse, ndipo iwo anagawira anthu achikunja chiyembekezo chakubwera kwa Mesiya. Mwa iwo amene Ayuda anaona ngati osapembedza ndi iwowo amene anali kumvetsetsa bwino mawu a chinenero onena zokubwera kwa Mesiya kuposa aphunzitsi a mu Israeli. Wena a iwo amene anali ndi chikhulupiriro cha kubwera kwa Yesu monga Mpulumutsi kuchokera ku tchimo, anayesetsa kuphunzira za chinsinsi cha chipembedzo cha Aheberi. Koma Ayuda pofuna kulimbikitsa mpatuko pakati pa iwo ndi mitundu ina, sanalikufuna kugawira nzeru zomwe anali nazo pa za nsembe. Otanthauzira oona, Mmodzi amene anaimira zimenezi, anayenera kubwera kudzazimasulira. Ziphunzitso ziyenera kupatsidwa kwa anthu muzinenero zawo. Yesu ayenera kubwera kudzafotokoza momveka bwino ndi kupatula choonadi ndi mawu opanda pake amene apangitsa choona kukhala mphamvu. Analipo ena pakati pa Ayuda amiyoyo yolimba amene anali kusungabe chiphunzitso cha Mulungu. Iwowa analimbikitsidwa m'chikhulupiriro chawo kupyolera mu chitsimikizo chimene anapatsidwa ndi Mose, “Ambuye Mulungu wanu adzautsa wina pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mumvere zonse zimene Iye akuuzeni.” Anawerenga m’mene Ambuye adzadzoza Mmodzi kuti “alalikire Uthenga Wabwino kwa ofatsa,” kuti “amange iwo osweka mtima, kukalalikira kwa am’nsinga kuti amasulidwe...ndikukalalikira za chaka chokomera Yehova.” Adzayenera “kukhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi” ndipo zisumbu “zidzalindira chilamulo Chake.” Amitundu adzabwera kwa kuunika Kwake, ndi mafumu kwa kuŵala kwa kutuluka Kwake. Machitidwe a Atumwi 3:22; Yesaya 61:1,2; 60:3; 42:4. Mawu a Yakobo pamene amafa anaŵadzaza iwo ndi chiyembekezo: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atabwera Silo.” Mphamvu yozimirira ya Aisraeli inachita umboni kuti kubwera kwa Mesiya kunali pafupi. Kunali chiyembekezo chofala kwambiri kuti kalonga wamkulu adzakhazikitsa ufumu wake mu Israeli ndipo adzabwera monga woombola wa amitundu. Genesis 49:10. M’mene Satana akanagonjetsera K UKWANITSIDWA KWA NTHAWI” kunafika. Kufooka kwa umunthu munthaŵi za uchimo, kunaitanira kudza kwa Mpulumutsi. Satana anayesetsa kupanga phompho lalikulu losatheka kudumpha pakati padziko lapansi ndi Kumwamba. Iye anaŵapanga anthu kuchita tchimo kopanda mantha. Chinali cholinga chake kupangitsa kupirira ndi kufatsa kwa Mulungu kuzilala kuti Iye ataye dziko lapansi m’manja mwa Satana. Zofuna za Satana kuti akhale wamkulu mwa onse, zinaoneka ngati zitheka. Ndizoona kuti mumbadwo uliwonse, ngakhale pakati pa achikunja, munali anthu amene kupyolera mwa iwo Khristu anagwira ntchito yotulutsira miyoyo ya anthu kuchoka mu uchimo. Koma anthu amenewa sanakondedwe. Ambiri a iwo anafa imfa yozunza. Mdima waukulu umene Satana anaika padziko lapansi unakulirakulirabe. Satana anapambana m’chigonjetso chake posokoneza chikhulupiriro cha Israeli. Achikunja anataya chidziŵitso cha Mulungu ndipo anachimwirachimwirabe. Chimodzimodzi ndi Israeli. Chikhulupiriro choti munthu angazipulumutse yekha kupyolera mu ntchito zake chimene chinakhazikitsidwa ngati maziko mu chikhulupiriro cha achikunja; chinasandukanso chikhulupiriro cha chipembedzo cha Ayuda. Mulungu Amvera Chisoni Dziko Lotayika A YUDA ANANYENGEZA DZIKO pakuphunzitsa chiphunzitso chonamachi. Iwo anakana kupereka miyoyo yawo kwa Mulungu ku chipulumutso cha dziko, ndipo anakhala iwo atumiki a Satana ku chiwonongeko cha dziko. Anthu amene Mulungu anaŵaitana kuti akhale zipupa ndi maziko a choonadi, anali kupanga zomwe Satana anafuna iwo kuti achite. Iwo anasankha kusaonetsera khalidwe la Mulungu moyenera, ndikupangitsa dziko lonse kumuona Iye ngati munthu oopsya ndi wodyerekera. Ansembe m’kachisi anataya tanthauzo la chipembedzo chomwe iwo analalikira. Iwo anali ngati anthu ochita seŵero. Mautumiki am'kachisi amene Mulungu anaŵasankha anapangidwa ndi ansembewa kukhala njira yopusitsira maganizo ndi kuumitsa kwa mitima ya anthu. Mulungu sakanapanganso kanthu kena kwa munthu kupyolera munjira zimenezi. Njira zonse zofooketsera mitima ya anthu zinali zitayamba kugwira ntchito. Mwana wa Mulungu, kuyang’ana m’dziko lapansi mwa chisoni, anaona anthu m’mene anatanganidwira ndi zofuna za Satana. Mosazindikira ndi mopusitsidwa, anali kuyenda mosasangalala m’njira ya imfa ku chiwonongeko chosatha kumene kulibe chiyembekezo cha moyo, ndiponso kuusiku umene kulibe m'dzukiro wa mam’maŵa. Matupi a anthu anasanduka mokhala ziŵanda. Maganizo, minyewa, zikhumbo za munthu ndi ziŵalo za anthu, zonse zinalamuliridwa ndi mphamvu yosaoneka yakuchita tchimo. Zizindikiro za usatana zinaonekera pankhope za anthu. Chibvundi choopsa nanga chimene Mombolo wa dziko anachiona. Tchimo linasanduka chiphunzitso cha pamwamba ndi choipa chinapatulikidwa kukhala mbali ya chipembedzo. Kupanduka ndi nkhwidzi za anthu zinalimbana ndi Kumwamba. Mayiko osagwa anali kuyang’anira Mulungu ndi chidwi kwambiri kuti awononge mitundu ya dziko lapansi. Koma ngati Iye akanapanga ichi, Satana anali okonzeka kupitiriza chilinganizo chake choŵanyenga anthu akumwamba kuti akhale mbali yake. Iye ananena kuti mfundo za boma la Mulungu zinali zosatheka kukhululukira. Ngati dziko lidakawonongedwa, iye akadamukanira Mulungu ndi kufalitsa mpatuko wake ku mayiko a Kumwamba. Koma m'malo mowononga dziko, Mulungu anatumiza Mwana Wake kudzalipulumutsa. Njira yolipulumutsira inaperekedwa. “Pamene nthaŵi inakwana”, Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu anatsira padziko lapansi mphamvu yachisomo yamachiritso imene singawonongedwe kapena kuchotsedwa kufikira chilinganizo cha chipulumutso chitakwanitsidwa. Yesu anabwera kubwezera mwa munthu chifanizo cha Mlengi wake. Kupirikitsa ziŵanda zimene zinali kulamulira chifuniro, kutinyamula m’mwamba kuchokera mfumbi, ndi kukonza makhalidwe athu onyansa kufanana ndi makhalidwe Wake wangwiro. |
Mutu 2 | Mutu 4 |