Angelo anafuna kuona m'mene anthu a Mulungu akadamulandirira Mwana Wake amene anabvala umunthu. Angelo anabwera kudziko limene kuwala kwa chinenero kunaonekera. Anabwera mosaoneka ku Yerusalemu ndi kwa awo otumikira m'nyumba ya Mulungu. Kudza msanga kwa Khristu nkuti kutalengezedwa kale kwa Zakaria mneneri pamene anali kutumikira m'kachisi. Wokonza njira ya Ambuye nkuti atabadwa kale, ndipo nkuti mbiri zake za kubadwa ndi cholinga cha ntchito zake zitafalitsidwa konsekonse. Koma Yerusalemu sanali wokonzeka kumulandira Mpulumutsi wake. Mulungu anaitana mtundu wa Chiyuda kuti uuze dziko za Ambuye kuti adzabadwa mufuko la Davide, koma sanadziwe kuti kudza kwake kwayandikira. Mukachisi, nsembe za mawa ndi madzulo zimalozera kwa Mwana wankhosa wa Mulungu, komabe sanakonzekere kumulandira Iye. Ansembe ndi aphunzitsi anapitiriza mapemphero wawo wopanda phindu ndi kutsatira njira zawo zopembedza, koma sanali kukonzeka kuchibvumbulutso cha Mesiya. Kunyalanyaza komweku kunadzaza mudziko lonse la Isaraeli. Mitima yadyera ndi yodzaza ndi zikondwerero za dziko, inali yosakhudzidwa ndi chisangalalo chomwe chinadzaza Kumwamba. Ochepa okha ndiwo anali ndi chidwi cha Osaonekayo. Angelo anali ndi Yosefe ndi Mariya pamene amayenda kuchokera ku Nazarete kupita kumzinda wa Davide. Lamulo la Aroma lolembetsa anthu onse linapita konsekonse muufumu wawo, kufikira ngakhale kumapiri a Galileya. Kaisara Augusto anali chiwiya cha Mulungu chobweretsa mayi Ake a Yesu ku Betelehemu. Mayi anali wa fuko la Davide, ndi Mwana wa Davide ayenera kubadwa mumzinda wa Davide. “Kuchokera mwa iwe [Betelehemu],” atero mneneri, “adzabwera...amene ati adzakhale oweruza mu Israeli; kubwera kwake ndiko kwa kale lomwe, kuchokera masiku osayamba.” Mika 5:2. Koma mumzinda wa wachifumuwu, Yosefe ndi Mariya anali wosazindikirika ndi wosalemekezeka. Otopa ndi opanda nyumba, anayenda kanjira kakang'ono chakum'mawa kwa mzinda, atalephera kufunafuna malo opumula usikuwo. Kunalibe malo kunyumba yogonera alendo. Kumapeto kwake m'nyumba ya chabechabe m'mene zinyama zimagona, anapeza malo opuma ndipo m'menemo Mpulumutsi anabadwa. Chikondwerero chinadzaza Kumwamba ndi mbiriyi. Olungama a maiko wena anadzaza ndi chidwi padziko lapansi. Mumapiri a Betelehemu gulu la angelo linadikirira chizindikiro kuti afalitse Uthenga Wabwino ku dziko lapansi. Atsogoleri mu Israeli akanakhala amodzi a ofalitsa mbiri ya kubadwa kwa Yesu Khristu, koma anadumphidwa. Kwa iwo amene akufuna kuwala nakulandira ndi chimwemwe, kuwala kochokera kumpando wachifumu wa Mulungu kudzawawalira. Onani Yesaya 44:3 ndi Masalimo 112:4. Ndi Abusa Okha Analabadira M 'THENGO M'MENE MNYAMATA Davide anaweta ziweto zake, abusa anayang'anira ndi kuyankhulana pamodzi usiku onse za lonjezano la Mpulumutsi ndi kupempherera za kudza Kwake. Ndipo “mngelo wa Ambuye anaimirira pakati pawo...Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope: pakuti onani, ndikuuzani inu Uthenga Wabwino wa chikondwerero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse. Pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.” Pamawu awa, masomphenya a ulemerero anadzaza maganizo a abusa amene anali kumvetsera. Mombolo wabwera! Mphamvu, ulemerero, chigonjetso, zalumikizana ndi kubwera kwake. Koma Angelo anawakonzetsera iwo kuti ayenera kuzindikira Mpulumutsi wawo waumphawi ndi wodzichepetsa: “Adzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona mukhola modyera ng'ombe.” Mtumiki wa Kumwamba anachotsa mantha awo. Iye anawauza iwo za m'mene angamupezere Yesu. Iye anawapatsa nthawi kuti azolowerane ndi kuwala kwake. Ndipo chigwa chonse chinawala ndi zikwizikwi za angelo a ulemerero wa Mulungu. Dziko linali la bata ndipo miyamba inaweramira kudziko lapansi kumvetsera ku nyimbo: Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba,O, mitundu yonse ikadazindikira lero nyimbo iyi! Liwu lake limene limamvekalo lidzakula mpaka ku malekezero anthawi ndi kumvekanso ku malekezero a dziko lapansi. Pamene angelo anazimira, mdima unabwereranso ku mapiri a Betelehemu. Koma chithunzi chowala chimene chinaonedwa ndi anthu chinakhalabe m'maganizo wa abusa. Iwo “anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelhemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife. Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Mariya, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera.” Atachoka ndi chimwemwe chachikulu, anazionetsera zinthu izo anazimva ndi kuziwona. “Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankula nawo.” Lero, Kumwamba ndi dziko lapansi sizinatalikirane monganso m'mene abusa anamvera nyimbo ya angelo. Angelo ochokera m'mabwalo a Kumwamba adzayenda nafe pamodzi kulikonse ndi paliponse. Munthano ya Betelehemu, zabisika “kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu!” Timadabwitsika ndi kudzipereka kwa Mpulumutsi wathu yemwe anasinthanitsa ulemerero Wake m'mwamba ndi modyera mwa n'gombe. Pamaso pa Iye kunyada kumatsutsidwa kwenikweni. Aroma 11:33. Koma izi zinali kuyamba chabe kwa kudzichepetsa Kwake. Uku kukanakhala kudzichepetsa kwake kwamuyaya kwa Mwana wa Mulungu pobvala umunthu ngakhale pamene Adamu anakhala muungwiro mu Edeni. Pamene dziko linakhala m'mabvuto a uchimo kwa zaka zikwi zinayi, Yesu analola kubvala umunthu. Monga mwana aliyense wa Adamu, Iye analola zotsatira za chilamulo cha chilengedwe chaanthu. Zotsatirazi zinaonetsedwa mu mbiri ya kale ya makolo Ake a pansi pano. Iye anadza ndi kutengera kwa chikhalidweku kuti tigawane mayesero athu ndi kutipatsa chitsanzo cha moyo wangwiro. Satana anadana ndi Khristu. Iye adamuzonda Iye amene anadzipereka kuombola ochimwa. Koma mudziko limene Satana anayikamo ufumu wake, Mulungu analola Mwana Wake kubwera monga waumphawi polephera pa mtundu wa anthu. Pokumana ndi choopsya cha moyo mofanana ndi moyo uliwonse, kumenya nkhondo monga m'mene mwana aliyense ayenera kumenyeramu choopsya chakulephera ndi chitayiko chamuyaya. Atate wa padziko lapansi amanjenjemera akayang'ana mwana wake naganizira za choopsya cha moyo. Amafuna kumuteteza iye kuchokera m'yesero ndi msautso. Chifukwa cha msautso wowawawu ndi zotsatira zoopsyazi, Mulungu anapatsa Mwana Wake wobadwa Yekha. “Chikondi chenicheni ndi ichi.” “Miyamba inu, dabwani! ndipo dziko, dzidzimuka!”
|