HOME |
Mutu 4 | Mutu 5 | Mutu 6 |
P ATAPITA pafupifupi masiku makumi anayi Yesu atabadwa, Yosefe ndi Mariya anamutenga Iye kupita naye ku Yerusalemu kukampereka kwa Ambuye ndi kukapereka nsembe. Monga mulowa m'malo wamunthu Khristu anayenera kumvera lamulo munjira iliyonse. Pomvera lamulo la Chiyuda Iye nkuti atadulidwa kale. Lamulo limafuna nsembe yopsyereza yankhosa monga yoyimira amayi, ndi nkhunda monga nsembe ya uchimo. Zoperekazi zinayenera kukhala zopanda mabanga popeza zimaimira Khristu. Iye anali mwana wa “nkhosa wopanda chilema ndi banga.” Iye anali chitsanzo cha m'mene Mulungu anamukonzera munthu kuti akhale wangwiro pa malamulo Ake. 1 Petro 1:19. Kuperekedwa kwa mwana woyamba wamwamuna kunayambidwa m'masiku oyambirira ambuyo. Mulungu analonjedza kupereka mwana woyamba wakumwamba kupulumutsa wochimwa Mphatso iyi inayenera kulandilidwa munyumba iliyonse popereka mwana wachisamba wamwamuna. Iye anayenera kuchita za unsembe monga woimira Khristu pakati pa anthu. Nanga kuperekedwa kwa Khristu kwa wansembe kunali ndi tanthauzo lanji. Koma wansembe sanathe kuona kupyola chophimba. Tsiku ndi tsiku amachita utumiki wamakanda osalabadira makolo ndi wana pokhapokha ataona kuti anali wolemera kapena apamwamba. Yosefe ndi Mariya anali wosauka, ndipo wansembe anangowaona ngati Agalileya obvala mwa wamba. Wansembe anatenga mwana m'manja mwake ndi kumunyamula patsogolo pa guwa la nsembe. Atampereka kwa mayi Ake, analemba dzina loti “Yesu” mubukhu. Pamene mwanayu anali m'manja mwake wansembe sanadziwe kuti anali kulemba dzina la Mfumu ya Kumwamba, Mfumu ya ulemelero, Iye amene anali chiyambi cha khalidwe lonse la Chiyuda. Mwanayu anali Iye amene anadzionetsera yekha kwa Mose kuti Iye anali INE. Iye anali Mtsogoleri wa ana a Israeli, amene anali mtambo wanthunzi masana ndi mtambo wamoto usiku. Anali Chilakolako cha mibadwo yonse, muzu ndi mbewu ya Davide, Nthanda ya M'mawa. Mwana wopanda thandizoyu anali Chiyembekezo cha mtundu wakugwa wa wanthu. Wakupereka dipo la machimo a dziko lonse lapansi. Koma ngakhale wansembe sanaone kapena kudziwa kanthu panthawi imeneyi, koma kanthu kena kanachitika kosonyeza Yesu. “Ndipo onani munali munthu mu Yerusalemu dzina lake Simeoni,... ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. Ndipo unamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaone Khristu Wake wa Ambuye.” Simeoni Wolemekezedwayo Anamuzindikira Yesu N DIPO PAMENE Simeoni analowa m'kachisi, anakhutitsidwa kwakukulu poona kuti mwana amene anali kuperekedwa kwa Ambuye anali Iye amene iwo anamuyembekezera kuti amuone. Ndipo wansembeyu anadabwa kwambiri naoneka ngati wodzidzimutsidwa. Anam'nyamula mwanayo m'manja mwake pamene mtsinje wa chimwemwe umene ndi kale lonse sanauone unali kuyenda mumtima mwake. Pamene ananyamula khanda la chipulumutsoli m'mwamba, anati “Ambuye, monga mwa mawu anu, tsopano lolani kapolo Wanu ndichoke mumtendere chifukwa maso anga aona chipulumutso Chanu chimene munakonza pamaso pa anthu onse kuunika kukhale chibvumbulutso cha kwa anthu amitundu ndi ulemerero wa anthu anu Israeli.” Pamene Yosefe ndi Mariya anali kudabwa ndi zolankhulidwazo iye anati kwa Mariya, “Taona, mwanayu waikidwa kuti akhale kugwa ndi kudzukanso kwa anthu ambiri mwa Israeli ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.” Nayenso m'meneri wamkazi, Anna, anafika panthawi yomweyo nabvomerezanso kutsimikizira umboni wa Simeoni. Nkhope yake inawala ndi ulemerero nathokoza kwa Mulungu kuti analoledwa kuona Khristu Ambuye. Iwo opembedza odzichepetsawa nawonso anaphunzira za mawu achinenero. Koma ngakhale atsogoleri ndi aneneri anali nawo uthenga wa mawu achinenero wopambana, iwo sanali kuyenda njira ya Ambuye ndipo maso awo sanathe kuona Kuwala kwa Moyo. Ndipo izi zilipobe. Chidwi cha m'mwamba monse chaikika pazinthu zimene zili zosazindikiridwa ndi atsogoleri a zipembedzo. Anthu amamudziwa Khristu mumbiri ya kale, koma Khristu muumphawi ndi m'mazunzo amene amadandaulira chithandizo, muntchito ya chilungamo imene imabweretsa kunyozedwa ndi umphawi, lero Iye sali olandilidwa ngati m'mene analili mu zaka mazanamazana zapitazo. Pamene Mariya anamuyang'ana mwanayo ali m'manja mwake, nakumbukira mawu amene analankhulidwa ndi abusa, iye anadzazidwa ndi chiyembekezo chowala. Mawu amene Simeoni adanena adamukumbutsanso iye mawu achinenero amene Yesaya adanena: “Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m'dziko lamthunzi wa imfa, kwatulukira kwa iwo...Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulunga wa mphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.” Yesaya 9:2-6. Mayi wa Khristu Ayenera Kubvutika K OMABE Mariya sanathe kumvetsetsa ntchito ya Khristu. Simeoni analosela za Iye monga kuunika kuti aunikire amitundu, ndipo Angelo analengeza za kubadwa kwa Mpulumutsiku monga chiyambi cha chimwemwe kwa anthu onse. Mulungu adalakalaka kuti anthu adzimuona Iye monga Mombolo wa dziko lonse. Koma zaka zambiri zinayenera kupita kuti mayi wa Yesu athe kumvetsetsa. Mariya sanaone ubatizo wa masautso umene mu ulamuliro wa Mesaya pa mpando wachifumu wa Davide unayenera kupambana. Mumawu a Simeoni kwa Mariya, “Lupanga lidzakupyoza iwe moyo wakonso,” Mulungu wachisomo anamuonetseratu mayi Wake wa Yesu m'sautso umene anayamba kukumana nawo chifukwa cha mwana wake. “Taonani,” Simeoni anati, “mwana uyu waikidwa akhale kugwa ndi kudzukanso kwa anthu ambiri mu Israeli.” Iwo amene ayenera kudzaukanso, ayenera kugwa. Tiyenera kugwa pathanthwe ndi kusweka tisanaukitsidwe mwa Khristu. Undekha uyenera kutayidwa. Ayuda sadakalandira ulemu umene umafikidwa kupyolera m'masautso. Choncho sanathe kulandira Mombolo wawo. “Kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.” Mukuwala kwa moyo wa Mpulumutsi, mitima ya onse, kuchokera kwa Mlengi ndi kwa kalonga wa mdima, imaululidwa. Mdyerekezi wamuonetsera Mulungu ngati wadyera. Koma mphatso ya Khristu imatsimikizira kuti pamene kudana kwa Mulungu ndi tchimo ndi kwa mphamvu monga imfa, komabe chikondi Chake kwa ochimwa ndi chozama koposa imfa! Atatha kutipezera chipulumutso, Mulungu adzatipatsa zonse zofunika ku matsilizidwe a ntchito Yake. Atatha kusonkhanitsa chuma chonse cha chilengedwe chonse, Anachipereka m'manja mwa Khristu, nanena, Gwiritsani ntchito mphatsozi ndi kuti mukamtsimikizire munthu kuti palibe chikondi chopambana choposa cha Ine. Ndikuti munthu adzapeza chisangalalo chachikulu chidzapazeke pakukonda Ine. M'mene Munthu Aliyense Adzadziweruzire Yekha P AMTANDA WA KALIVALE, chikondi ndi kudzikonda zinayang'anana maso ndi maso. Moyo wa Khristu unali wosangalatsa ndi wodalitsa anthu, ndipo kumupha Iye, Satana anaonetsera udani wake ndi Mulungu. Cholinga chenicheni cha kuukira chinali kulanda ufumu wa Mulungu ndi kuwononga Iye amene kupyolera mwa Iye chikondi cha Mulungu chinaonekera. Mu m'moyo ndi m'imfa ya Khristu, maganizo a anthu amaonetsedwa poyera. Moyo wa Yesu unali kuitanira anthu kwa kudzikana ndi kuyanjana naye m'mabvuto. Onse amene amamvetsera Mzimu Woyera anadza kwa Iye. Wopembedza a undekha anali kudziika okha ku ulamuliro wa Satana. Mumachitidwe awo kwa Yesu, wonse amasonyeza mbali imene iwo anali. Ndipo aliyense amadziweruza yekha. Patsiku la chiweruzo chotsiriza, mtanda udzaonetsedwa ndipo cholinga chake chidzaonekera kwa munthu aliyense. Patsogolo pa masomphenya a mtanda ndi wokanthidwayo ali pompo, ochimwa onse adzaima ali otsutsidwa Anthu adzaona zotsatira za kusankha kwawo. Funso lililonse lamunkanganowu lidzakhala litayankhidwa bwinobwino. Mulungu sadzadzudzulidwa chifukwa cha chikhazikitso ndi m'chitidwe wa uchimo. Kudzaonetsedwa kuti boma la Mulungu linalibe bvuto lina lililonse ndipo siliyenera kutsutsidwa. Onse omvera ndi oukira adzati “Njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha...zolungama zanu zidaonetsedwa.” Chibvumbulutso 15:3,4. |
Mutu 4 | Mutu 6 |