HOME
Mutu 5 Mutu 6 Mutu 7
Taona Nyenyezi Yake

Y ESU ATABADWA mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herodi mfumu, toanani panabwera anzeru akum'mawa, nanena, 'Ali kuti Iye amene wabadwa mfumu ya Ayuda? Ife taona nyenyezi Yake kum'mawa ndipo tadza kudzamlambira Iye.' ”
     Anzeru akum'mawa anali am'gulu la achuma ndi ophunzira. Pakati pawo panali anthu oona mtima amene anaphunzira choonadi kupyolera m'chilengedwe ndipo Mulungu analemekeza kuona mtima kwawo ndi nzeru zawo. Anthu anzeru zoterezi ndiwo amene anabwera ku Yerusalemu kudzaona Yesu.
     Pamene anthu anzeruwa anali kuphunzira za nyenyezi m'mwamba, anaona ulemelero wa Mlengi. Pofuna chidziwitso chowonjezekera, anatsegula mabuku a Chiheberi. Pakati pa dera lawo lomwelo zinalipo zolembera za chinenero zomwe zidalosera za kubwera kwa mphunzitsi woyerayo. Chuma cha ulosi wa Balamu chakhala chili kulandiridwa kuchokera ku mbadwo umodzi kupita ku unzake. Muchipangano chakale anzeru akum'mawa mwa chisangalalo adadziwa kuti kubwera kwa Mpulumutsi kunali pafupi. Dziko lonse linayenera kudzadzidwa ndi chidziwitso cha ulemelero wa Ambuye.
     Usiku umenewo, anzeru akum'mawa adaona kuwala kodabwitsa m'mwamba pamene ulemelero wa Mulungu unasefukira m'mapiri a Betelehemu. Nyenyezi yowala modabwitsa inawaonekera niima mlengalenga chooneka chomwe chidakondweretsa zofuna zawo. Nyenyeziyo yinali gulu la angelo onyezimira koma izi anzeruwa sanazizindikire. Koma anali okhutitsidwa kuti nyenyeziyo yinali yofunikira kwambiri kwa iwo. Kodi nyenyezi yodabwitsayi idatumizidwa monga chidziwitso cha Olonjezedwayo? Anzeruwa anakulandira kuwala kwa choonadi chochokera Kumwamba; tsopano kunawawalira kwa thunthu. Kupyolera m'maloto anauzidwa kuti akafune kalonga amene wangobadwa kumeneyu. Onani Numeri 24:17.
     Dziko la kum'mawa linali ndi zinthu zambiri za pamwamba, ndipo anzeru atatuwo sanakaone mwanayo chimanjamanja. Mphatso za pamwamba zamdziko zimaperekedwa monga zopereka kwa Iye amene mwa Iye mabanja onse a padziko akanadalitsidwa.

Ulendo Wa Usiku
K UNALI KOFUNIKA KWAMBIRI kuyenda ulendo wawo nthawi yausiku kuti adzitha kutsogozedwa ndi nyenyezi, koma paliponse pamene anapuma aulendowa anafufuza m'malemba. Iwo anali wokwanitsidwa ndi wokhutitsidwa kuti anali kutsogozedwa ndi Mulungu. Ulendowu ngakhale unali wautali, unali wokondweretsa ndi wosangalatsa.
     Iwo anafika mu dziko la Israeli, ndipo Yerusalemu ataonekera. Anaona nyenyezi itaima pamwamba patsindwi la kachisi. Moyenda ndi chisangalalo ndi mphamvu anapita chitsogolo ndi chikhulupiriro chodzaza nayembekezera kuti kubadwa kwa Mesiya kukhala katundu wa chimwemwe kwa lilime lililonse. Koma chodabwitsa nchakuti, mafunso awo sanatulutse chimwemwe mwa anthu koma kudabwa ndi mantha zosakanikirana ndi kunyoza.
     Ansembe analankhula motamandira chipembedzo chawo nadziwerengera okha, nanyoza Aherene ndi Aroma monga ochimwa. Anzeru akum'mawa sanali anthu opembedza mafano, ndipo pamaso pa Mulungu anzeru akum'mawa anali oposa osankhika ake amulunguwa, komabe Ayuda amawaona iwowa ngati anthu akunja. Kufunsa kwawo kofuna kudziwa zambiriku sikunawapange Ayuda kuwamvera chisoni ndikuwathangata kuti amvetsetse.

Nsanje Ya Herodi Iwonekera
U LENDO WODABWITSA wa anzeru akum'mawa unadzetsa kuzizwa mu Yerusalemu ndipo kuzizwaku kudapitirira mpaka kunyumba ya mfumu Herodi. Chiwembu cha Herodi chinadza poona kuti ufumu wake ungakhale wolimbanirana chifukwa anachokera kufuko la a Edomu. Pokhala wamfuko lina, iye anazondedwa ndi anthu; chitetezo chake chinali chochokera ku Roma. Koma Kalonga watsopanoyu anali ndi ulamuliro waukuklu. Iye anabadwa muufumu umenewu.
     Herodi anayesa kuti ansembe pamodzi ndi alendowo anakonza chiwembu choti alande mpando wake. Ndi chitsimikizo chofuna kutsekereza zimene amaganizazo, iye anawaitana ansembe ndi kuwafunsa iwo zakumalo kumene Mesiya anabadwira.
     Kufunsa kwa Herodi kumene anafunsa kwa alendo kunapangitsa aphunzitsi Achiyuda kuwawidwa mtima. Mosalabadira anafutukula malembo awo a chinenero mowawidwa ndi nsanje yaikulu koti mfumu yansanjeyo inakwiya kwambiri. Iye anaganiza kuti iwo amamubisira choonadi chomwe amachidziwa. Ndi ulamuliro umene iwo sanakatha kuukana anauzidwa ndi Herodi kuti amuke, akafunefune ndi kudzamuuza malo amene mfumu woyembekezedwayo anabadwira. “Ndipo anati kwa iye, Ku Betelehemu wa Yudeya: Pakuti kwalembedwa ndi aneneri,
Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya,
Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya.
Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe
Amene adzaweta anthu anga Aisraeli.

     Tsopano Herodi anaitana anzeru akum'mawawa kumafunso amseri. Ukali ndi mantha zinayendayenda mumtima mwake koma anaonetsa chiphamaso naonetsa ngati anali ndi chionetsero chofuna kutamanda kubadwa kwa Khristu. Iye anawapempha alendewo kuti, “Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mawu, kuti nanenso ndidzadze kudzamlambira Iye.”
     Ansembe sanali onga m'mene iwo amachitiramu. Uthenga wonena za maonekedwe a angelo kwa abusa unamveka mu Yerusalemu koma aphunzitsi anauona ngati chidziwitso chopanda pake. Iwo akadakhala ali okonzeka kuperekeza anzeruwo kumalo komwe kudabadwira Yesu, koma m'malo mwake, anzeru akum'mawawo ndiwo amene anadziwitsa iwo za kubadwa kwa Mesiya.
     Ngati zonena za abusa ndi anzeru akum'mawawo zinalikuoneka zopambana ndi zoona pamaso pa ansembe, iwo akadatsutsa ansembe omwe amadzitamandira kuti amadziwa choonadi cha Mulungu. Aphunzitsi odziwawa sanafune kuti alangizidwe ndi anthu achikunja. Iwo anaganiza kuti sizingatheke kuti Mulungu anawapitirira iwo nakalankhulana ndi abusa wosadziwawo kapena amitundu wosadulidwawo. Iwo sanapite konse ku Betelehemu kuti akaone ngati izi zinali choncho. Ansembewa anapotoza anthu kuti adziona kuti kubadwa kwa Yesu kunali kongopatsa chiphwete. Pano ndi pamene ansembe ndi aphunzitsi anayamba kumkana Yesu. Kunyada ndi kuumitsa mitima kwawo kunakula mpaka kunapanga maziko a udani pa Mpulumutsi.
     M'kachisisira kamadzulo anzeru akum'mawawo anatuluka mu Yerusalemu okhaokha. Ndi chisangalalo anaionanso nyenyezi ija ndipo anatsogozedwa ku Betelehemu. Pokhumudwa ndi kusalabadira kwa atsogoleri a Chiyuda, iwo anachoka mu Yerusalemu ndi chikaiko koposa m'mene iwo anafikamo.

Popanda Alonda a Mfumu
K U BETELEHEMU, sanapeze alonda achifumu woti alondere mfumu yobadwa tsopanoyi. Panalibe munthu wotchuka ndi m'modzi yemwe amene anafikako. Yesu anamugoneka modyera mwa ng'ombe, nayang'anidwa ndi makolo Ake okha. Kodi uyu akadakhala iye amene “adzautse mafuko a Yakobo” ndi “kudzakhale kuunika kwa amitundu” ndi “chipulumutso mpaka kumalakezero a dziko?” Yesaya 49:6.
     “Iwo atalowetsedwa munyumba, anaona mwana ali ndi Mariya mayi Wake ndipo anagwa pamaondo awo namulambira Iye.” Ndipo anatulutsa mphatso zawo nampatsa Iye mitulo ndiyo “golidi, libano ndi mure.” Chikhulupiriro nanga cha anzathuwa!
     Anzeruwa posadziwa maganizo a Herodi, anaganiza zoti adzere ku Yerusalemu kuti akamtsimikizire kuti mfumu ija anaipeza. Koma m'maloto iwo anadziwitsidwa zoti asadzere kukaonana naye. M'malo modzera ku Yerusalemu, iwo anadzera njira ina napita kudziko la kwawo.
     Yosefe nayenso analandira chenjezo loti athawire ku Iguputo ndi Mariya ndi mwana wake. Yosefe anamvera, popanda kuchedwa nanyamuka usiku ndi cholinga chodzipulumutsa.
     Kufunsa kwa anzeru akum'mawa mu Yerusalemu, chidwi cha kukondwerera pa zofuna za anthu, ndi nsanje ya Herodi, zinapangitsa kuti ansembe ndi aphunzitsi akhale atcheru pokumbukira m'maganizo mwawo ku zinenero zonenera Mesiya ndi zinthu izo zazikulu zinachitika.
     Satana pofuna kutseka kuwala kwa Mulungu kuti kusafike padziko, mochenjera ndi nzeru iye anafuna kuwononga Mpulumutsi. Koma Iye amene sasinza kapena kugona anapereka populumukira pa Mariya ndi mwana Yesu kudziko la chikunja. Kupyolera m'mphatso za anzeru akum'mawa, Mulungu anawapatsa njira yam'mene angachitire paulendo wopita ku Iguputo ndi kukakhala mongoyembekezera akudziko la chilendo.

Choopsya cha Herodi
K U YERUSALEMU, Herodi anakhala akuyembekezera anzeru akum'mawa. Kukayika kwake kumayamba kukula pamene nthawi inayamba kupita ndikuti iwo sanaoneke. Kodi ansembe analowa m'maganizo ake nanga kodi anzeru akum'mawawa adamlambalala dala? Ndi ganizo ili maganizo ake adapenga. Kupyolera mu chikakamizo iye akadapanga chitsanzo pa mwana uyu wachifumu.
     Asilikali anatumizidwa ku Betelehemu kuti akaphe ana onse a zaka ziwiri kapena kucheperapo. Nyumba za phee zamzinda wa Davide zinachitira umboni izo zimene zinaloseledwa zaka mazana asanu ndi chimodzi zapitazo. “Mawu anamveka m'Rama, Maliro ndi kuchema kwambiri: Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.”
     Ayuda anadzibweretsera masautsowu pa iwo eni. Iwo anakana Mzimu Woyera, womwe unali chishango chawo chenicheni. Iwo anafunafuna maulauli womwe akanamasulira modzikweza iwo okha ndi kuonetsa m'mene Mulungu amanyozera mitundu ina. Chinali chiyembekezo chawo kuti Mesiya anayenera kudza monga mfumu napondereza amitundu ndi mkwiyo Wake. Ndipo izi zinapangitsa udani wa atsogoleri awo. Kupyolera mu kusaonetsedwa bwino kwa ntchito ya Yesu, Satana anakonzetsera chiwonongeko cha Mpulumutsi; koma m'malo mwake zinawatembenukira iwo omwe.
     Ana osachimwawa atangophedwa, Herodi anafa imfa yoopsya. Yosefe, yemwe panthawiyi anali ku Iguputo anauzidwa ndi mngelo kuti abwerere ku Israeli. Poona Yesu monga mulowa m'malo wa ufumu wa Davide, Yosefe anafuna kumanga nyumba yake ku Betelehemu; koma pakumva kuti Arikelawo anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herodi, anachita mantha kupita kumeneko naganiza kuti mwina iyeyo angakwaniritse cholinga cha atate wake.
     Yosefe anasonyezedwa kumalo kothawirako kwawo kwakale ku Nazarete. Uku ndikumene Yesu anakhala pafupifupi zaka makhumi atatu “kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti adzachedwa Mnazarayo.” Ku Galileya kunali mitundu yosiyanasiyana ya anthu akudza kusiyana ndi ku Yudeya; ndiye panalibe chidwi chenicheni mu zinthu zokhudzana ndi chiyuda.
     Umu ndimomwe Mpulumutsi analandiridwira pamene Iye anadza kudziko lapansi. Mulungu sanamsiyire munthu wina aliyense udindo woyang'anira Mwana Wake wokondedwa paanthu, ngakhale pamene anali kukonza ntchito Yake ya chiombolo cha anthu. Mulungu analamula angelo kuti asamale ndi kuteteza Yesu mpaka atakwaniritsa cholinga Chake nafera m'manja mwa iwo amene anadzera kudzawapulumutsa.

Mutu 5 Mutu 7