HOME |
Mutu 6 | Mutu 7 | Mutu 8 |
Y ESU MU UBWANA ndi unyamata wake anakhala kumudzi wamng'ono wa m'mapiri. Iye anadutsa nyumba zolemera ndi awo amene anali aphunzitsi odziwika ndi cholinga chofuna kupanga Nazarete mudzi Wonyozekawo Kwawo. N DIPO MWANA ANAKULA, mumzimu, ndi munzeru ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye." Mu kuwala kwa Bambo Wake, Yesu "anakulabe m'nzeru ndi munsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu." Maganizo Ake anali achangu, akuya, ndi anzeru koposa zaka zake. Mwa pang'onopang'ono nzeru za kuganiza zinakula mwa Iye potsata malamulo a umwana. Luka 2:52. Monga mwana, Yesu anali wansangala, anaonetsa kufatsa kozama ndi kuona mtima koonetsera kukhulupirika. Mwa nji! ngati mwala, moyo Wake unaonetsera khalidwe la ulemu wopanda dyera. Mayi Ake a Yesu anaona luntha la mphamvu Zake nafuna kulimbikitsa maganizo Ake ololera anzeruwo. Kupyolera mwa Mzimu Woyera, iye analandira m'nzeru zolumikizana ndi atumiki a Kumwamba pa kukula kwa mwana uyu amene anaona Mulungu Yekha monga Atate Wake. Mu masiku a Khristu, malangizo a uzimu a kwa wana anali amwamba. Anthu anakonda miyambo yawo kuposa Malemba. Maganizo anali wodzazidwa ndi zinthu zimene sizikanabvomerezedwa musukulu ya Kumwamba. Asikolala sanapeze ola la phee! lokhala ndi Mulungu kumva mawu Ake akuyankhula kumitima yawo. Iwo anafulatira kasupe wa nzeru. Izo zimene zimatengedwa ngati "zopambana" m'maphunziro zinali chopysinja chachikulu ku kukula kwa anyamata ndi asungwana. Maganizo awo anali wosokonezeka ndi wochepa. Mwana Yesu sanalandire malangizo a mu sukulu za mu sunagogi. Koma kuchokera kwa mayi Ake ndi zolemba za aneneri, Iye anaphunzira za zinthu za Kumwamba. Pamene anali kukula mu unyamata Wake, Iye sanafune sukulu za aphunzitsi achirabi. Iye sanafune chiphunzitso chochokera mu magwero amenewa. Iye podziwa ndi kuzolowerana kwambiri ndi Malembo, zikusonyeza m'mene Iye amaphunzirira mawu a Mulungu ali wamng'ono. Za M'baibulo Ziwonjezeredwa ndi Chilengedwe M ASO AKE anatsegulira kunkhokwe ya zinthu zolengedwa ndi Mulungu. Iye amene anapanga zinthu zonse anaphunzira maphunziro a zimene manja Ake analemba padziko, panyanja ndi mulengalenga. Anasonkhanitsa nzeru za kuya kuchokera ku chilengedwezomera, nyama ndi munthu. Mafanizo amene Iye anakonda kuphunzitsira maphunziro a choonadi amasonyeza m'mene Iye amasonkhanitsira maphunziro a uzimu kuchokera ku chilengedwe ndi zinthu zomuzungulira tsiku ndi tsiku. Pamene Yesu amayesa kumvetsetsa chifukwa cha zinthu, angelo ndiwo amene amamuthandiza Iye. Kuchokera pamene anayamba kuzindikira zinthu, Amakula nthawi zonse muchisomo cha uzimu ndi nzeru za choonadi. Mwana aliyense angapeze nzeru monga m'mene anachitira Yesu. Pamene tikukhala ozolowerana ndi Atate wathu wa Kumwamba, angelo adzakhala pafupi nafe, maganizo athu adzakhala olimbikitsidwa, makhalidwe athu adzaongoledwa ndi kukonzedwa. Tidzakhala pafupifupi ngati Mpulumutsi wathu. Pamene tikuona zinthu zikuluzikulu zokongola za m'chilengedwe, chikondi chathu chidzamtsata Iye. Mzimu umapatsidwa ulemu, moyo umapatsidwa mphamvu polumikizana ndi Wosatha kupyolera muntchito Zake. Kulumikizana ndi Mulungu mupemphero kumakulitsa maganizo ndi kusankha kwa umunthu. Yesu ali mwana amaganiza ndi kulankhula monga mwana, koma panalibe banga la uchimo lomwe linawononga chithunzi cha Mulungu mwa Iye. Koma Iyeyu sikuti anali pamtambasale wopanda mayesero. Anthu a mu Nazareti anali otchuka ndi uchimo wawo. Kunali kofunikira kuti Yesu adzisamalira mzochita zake kuti asunge ungwiro Wake. Anakumana ndi mabvuto onse amene timakumana nawo, kuti akhale chitsanzo chathu mu umwana, unyamata ndi ukulu. Onani Yohane 1:46. M'zaka zoyambirira za moyo Wake, Iye amalonderedwa ndi angelo akumwamba, koma moyo Wake unali wa nkhondo ndi mphamvu za mdima nthawi zonse. Kalonga wa mdima anayesa njira zosiyanasiyana kuti amchimwitse Yesu ndi yesero. Yesu anazolowerana bwinobwino ndi umphawi, nadzikana yekha nasowa womusangalatsa. Chizolowezi ichi chinali tchinjirizo kwa Iye. Analibe nthawi yonyenya yoti ikadamutsogolera kumagulu azisokonezo. Phindu ngakhale chisangalalo, kuyamikidwa ngakhale kudzudzulidwa zonsezi sizinampange Iye kuti alakwe. Khristu, munthu mmodzi yekha wosachimwa amene anakhala padziko, pafupifupi zaka 30 anakhala pakati pa anthu ochimwa a mu Nazareti. Izi zinali chidzudzulo kwa iwo amene amaganiza okha kudalira pamalo, chuma ngakhalenso chipambano kuti akhale moyo wopanda zifukwa. Monga M'misiri wa Matabwa Khristu Analemekeza Ntchito Y ESU ANALI WOLAMULIRA WA KUMWAMBA, ndipo angelo anakondwerera kukwaniritsa mawu Ake; tsopano anali kapolo wolola, wokonda ndi mwana womvera. Ndi manja Ake anagwira ntchito pamalo opalira matabwa ndi Yosefe. Iye sanagwiritse ntchito mphamvu za Atate Wake kuti achepetse mazunzo kapena kupeputsa ntchito Yake yolemetsayo. Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu za umunthu munjira yodzisungira thanzi, kuti athe kugwira ntchito mopambana. Sanalole kuti akhale wolephera ngakhale pa kagwiridwe ka zida za matabwa. Iye anali katswiri pantchito Yake monga m'mene makhalidwe Ake analili. Pachitsanzo, Iye anaphunzitsa kuti ntchito iyenera kugwiridwa molunjika ndi mwamphumphu ndi kuti ntchito ndiyolemekezeka. Mulungu anasankha ntchito monga dalitso ndipo ndi yekhayo wantchito wokhulupirika amene amapeza ulemelero weniweni ndi chisangalalo cha moyo. Chitsimikizo cha Mulungu chimakhala pa ana ndi anyamata amene amatenga mbali pantchito za panyumba kuthandizana mabvuto a mayi ndi bambo. Yesu anali wofulumira ndi wogwira ntchito mosatopa. Amayembekezera zambiri chonchonso amayesa kuchita zambiri. Anati "Ndiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito." Yesu sanakane chisamaliro ngakhale udindo ngati m'mene amachitira anthu amene amadzitcha kuti ndi omutsata Iye. Chifukwa ambiri amafuna kuzemba kusunga mwambo, kwa iwo ambiri ndi ofooka, osakwanitsa, amantha, ndi ooneka opanda ntchito akakhala m'mabvuto. Chitsimikizo ndi mphamvu za makhalidwe zimene zinaonetsedwa mwa Khristu zinayeneranso kukula mwa ife kupyolera mumkusunga mwambo momwe Iye anapitirira. Chisomo chimene Iye analandira ndi cha ife. Yohane 9:4. Mpulumutsi wathu anagawana nawo wosauka. Iwo amene analandira moyo wake wosatha kotheratu, sadzamva kuti olemera anayenera kulemekezedwa kuposa osauka. Woyimba Wa Chimwemwe N THAWI ZAMBIRI Yesu amasonyeza chisangalalo cha mumtima Mwake poyimba masalimo ndi nyimbo za Kumwamba. Kawirikawiri mbadwa za mu Nazareti zimamva mawu Ake opfuula poyamika ndi nyimbo. Pamene anzake anali kudandaula zotopa, amasangalatsidwa ndi mawu anthenthemya ochokera mkamwa Mwake. Kuchokera mu zaka Zake za ku Nazareti, moyo Wake unali wachisoni ndi wachikondi. Akulu, achisoni, olefuka ndi uchimo, ana osewera, zilengedwe zazing'onozing'ono ndi zilombo zofatsa zamlengalenga zinali zokondwa kukhala naye. Iye amene anapanga maiko onse ndi mawu, Iyenso anawerama ndi kusamalira mbalame yachironda. Panalibe chimene chidakamuimitsa Iye kutumikira. Chotero Iye anakula munzeru ndi munsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi munthu. Iye anadzisonyeza kumva chisoni ndi onse. Chikhulupiriro ndi kulimba moyo kumene anali nako, kunapangitsa dalitso m'nyumba zonse. Kawirikawiri pa Sabata anali kuitanidwa kukawerenga phunziro la aneneri, ndipo mitima yaomvetsera inaona kuwala kooneka kuchokera mu Malemba. Komabe pazaka zonse anali ku Nazareti, sanaonetsere mphamvu zozizwitsa mwa Iye yekha. Iye sanafune kutchulidwa mu udindo Wake. Moyo Wake wa phee! ndi wozichepetsa ukutiphunzitsa phunziro lofunika kwambiri. Pamene mwana sakhala womasuka kuzikondwerero zopanda pake, namakonda kuphunzira chilengedwe, iye amadzakhala wamphamvu, m'maganizo ndi mu uzimu. Yesu ndiye chitsanzo chathu. M'moyo wa m'nyumba mwawo unali chitsanzo choyenera kuchitsatira kwa ana ndi achinyamata onse. Mpulumutsi anazichepetsa ngati waumphawi, kuti atiphunzitse m'mene ife mu usauki tingathe kuyenda ndi Mulungu. Ntchito Yake inayamba pakulemekeza umisiri umene umatchedwa wapansi umene anthu ake amagwira ntchito tsiku ndi tsiku kuti apeze chakudya. Pamene anali kugwira ntchito yopala matabwa anachita ntchito ya Mulungu monganso pamene anachita zozizwitsa kwa anthu ambiri chifukwa ntchito zonsezi ndizofunika pamaso pa Mulungu. M'nyamata aliyense amene amatsatira chitsanzo cha Khristu cha kukhulupirika, ndi kumvera munyumba mwawo, adzamva mawu awa, wonenedwa ndi Atate: "Taona, Mtumiki Wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika Wanga, amene Moyo Wanga ukondwera naye." Yesaya 42:1. |
Mutu 6 | Mutu 8 |