HOME |
Mutu 7 | Mutu 8 | Mutu 9 |
P AKATI PA AYUDA mwana akafika chaka cha khumi ndi chiwiri chinali malire a umwana ndi unyamata. Potsata mwambowu, Yesu anapita ku Yerusalemu ku Pasika ndi Mariya ndi Yosefe Iyeyo atakwana Msinkhu Woikikawu. U LENDO WOCHOKA ku Galileya umatenga masiku ambiri; ndipo aulendowo amayenda mu magulumagulu pofuna chitetezo. Chifukwa cha misewu yoipa amayi ndi abambo okalamba amakwera pa bulu kapena pa galeta. Amuna ndi anyamata amphamvu amayenda pansi. Dziko lonse limakongola kwambiri chifukwa cha maluwa owala ndi mbalame zoimba bwino. Munjira amayi ndi abambo anayamba kufotokoza kwa ana awo zodabwitsa zimene Mulungu anachitira anthu ake mu zaka za m'mbuyomu nasangulutsa ulendo ndi nyimbo ndi mabvume. Kusunga kwa tsiku ili kunayambika ndi mbiri yobadwa kwa mtundu wa Chiheberi. Pa usiku wotsiriza womwe iwo anatuluka mu ukapolo wa ku Iguputo, Mulungu analamula a Heberi kuti asonkhanitse mabanja awo m'nyumba zawo. Atatha kuwaza mwazi wa mwana wophedwa wa nkhosa pamphuthu pa makomo awo, iwo anayenera kudya nkhosayo, yootchedwa, ndi mkate wopanda chotupitsa ndi ndiwo zowawa. "Ndiye Pasika wa Ambuye." Pakati pa usiku, onse oyamba kubadwa a mu Iguputo anaphedwa. Ndipo Aheberi anachoka m'Iguputo ali mtundu wa ufulu. Kuchoka kum'badwo kufika kum'badwo wina nkhani ya chiombolo chodabwitsachi inayenera kubwerezedwabwerezedwa. Onani Eksodo 12:11. Pasika amatsatana ndi masiku 7 a phwando la mkate wopanda chotupitsa. Machitidwe a phwando anali kuonetsera mitundu ya ntchito ya Khristu. Nkhosa yophedwa, mkate wopanda chotupitsa, zipatso zowundukula, zonsezi zimaimira Mpulumutsi. Koma anthu ambiri m'masiku a Yesu amauona m'chitidwe wa phwandowu monga mwambo chabe wopanda ntchito. Nanga izi zimaimiranji kwa mwana wa Mulungu! Kwa nthawi yake yoyamba mwana Yesu anaona kachisi. Anaona ansembe amikanjo yoyera akuchita mautumiki awo mokhudza mtima, nkhosa yoperekedwayo ili pa guwa lansembe. Iye anaonerera ndi chidwi miyambo ndi chilinganizo cha Pasika. Tsiku ndi tsiku Iye anaona tanthauzo lake la zonsezi bwinobwino. Chochitika chilichonse chinaoneka cholozera kumoyo Wake. Maganizo atsopano anabadwa mwa Iye. Mwa chete ndi nkukhudzidwa, anaoneka ngati ali kuphunzira ndi kumvetsetsa chibvuto chachikulu. Chozizwa cha ntchito Yake chinayamba kufutukuka kwa Mpulumutsi. Pokutidwa ndi maganizo ozama a zinthu izi, pamene mwambo wa Pasika unatha, Iye analowa kumpanda wa kachisi, ndipo pamene wolambirawo anabalalika kuchoka ku Yerusalemu, Yesu anasiyidwa mbuyo. Pa ulendo umenewo makolo a Yesu anafuna kuti mwana wawo okakumane ndi aphunzitsi a pamwamba a mu Israeli. Iwo anayembekezera kuti angakaphunzitsidwe Iye kuchitira ulemu aphunzitsiwa ndi kusunga ziphunzitso zawo. Koma Yesu mukachisi muja anaphunzitsidwa ndi Mulungu. Izo zimene analandira kuchokera kwa Mulungu anayamba kuzigawa nthawi yomweyo. Chipinda chimene chinalumikizana ndi kachisi chinapangidwa kukhala sukulu ya zauzimu. Mmenemu mwana Yesu anadza nakhala pansi pamodzi ndi aphunzitsi anzeruwa. Monga munthu wofuna nzeru, Iye anafunsa aphunzitsiwa molingana ndi mawu a chinenero ndi zinthu zimene zikuchitika kulozera ku zozizwa za kubwera kwa Mesiya. Mafunso Ake amaulula choonadi chakuya, zobisika zakale zimene zinali zofunika ku chipulumutso. Poonetsa kuchepa ndi kufupika nzeru kwa aphunzitsi anzeruwa, funso lililonse linaonetsera choonadi chilichonse monga mmene chinayenera kuonedwera. Aphunzitsi analankhula za zinthu zopambana zimene Mesiya akadabweretsa kwa Ayuda; koma Yesu anaonetsera ulauli wa Yesaya nafunsa tanthauzo la zolembera zimene zimalozera ku mabvuto ndi imfa ya Mwana Wankhosa wa Mulungu. Onani Yesaya 53. Asing'anga anadza kwa Iye ndi mafunso ndipo anadabwitsika ndi mayankho Ake. Mozichepetsa monga mwana, Iye anapereka malembo a tanthauzo lenileni limene anzeru sanalikulidziwa. Akadatsatira choonadi chimene chinanenedwacho akadasintha ndi kukonzanso chipembedzo cha masiku awo; ndipo pamene Yesu anayamba ntchito Yake yolalikira, ambiri akadakhala atakonzeka kumulandira Iye. Mwa m'nyamata uyu wa maganizo akuthwa wa Chigalileyayu, aphunzitsi anazindikiramo tsogolo lopambana. Iwo anafuna kuti amuphunzitse mwanayu kuti maganizo Ake akuthwawa adzazidwe ndi ziphunzitso zawo. Mawu a Yesu anagwedeza mitima yawo imene ndi kale lonse siinagwedezekepo ndi mawu amene amachokera pa lilime la munthu. Mulungu analikufuna kupereka kuwala kwa atsogoleriwo. Ngati Yesu akanaoneka ngati kuti akufuna kuwaphunzitsa aphunzitsiwo, iwo akadayesa zopanda pake kuti amvere. Iwo anadzinamiza okha naganiza kuti amamuphunzitsa Iye kapena kuti amayesa nzeru Zake za m'malembo. Kudzichepetsa ndi ulemu wa kamnyamataka Yesu kudachotsa ganizo lomunyoza. Mitima yawo inatsegulira ku Mawu a Mulungu ndi Mzimu Woyera analankhula kumitima yawo. Iwo anatha kuona kuti chiyembekezo chawo pa Mesiya sichinali kugwirizana ndi mawu a chinenero, koma sanathe kubvomera kuti sanathe kumvetsetsa malembo amene amaphunzitsawa. Makolo Ake Adandaula P AMENE Mariya ndi Yosefe anachoka m'Yerusalemu, Yesu anawasokonekera. Chisangalalo choyenda ndi abwenzi chinatenga chidwi chawo, ndipo sanazindikire kusoweka kwake mpaka m'mene usiku unafika. Ndipo anasowa dzanja la chithandizo cha mwana wawo. Poganiza kuti Iye anali m'gulu lawo lomwelo, analibe nkhawa. Tsopano mantha anabadwa m'mitima yawo. Ataganiza mwakuya, anakumbukira m'mene Herodi anafunira kumuwononga Iye muukhanda wake. Ndingaliro zoopsya zinadzaza mitima yawo. Atabwerera ku Yerusalem, anapitiriza kufuna kwawo. Tsiku lachiwiri lake, m'kachisi, mawu odziwika a Yesu anamveka kwa iwo. Sanawaphonye mawuwo amene anali a mphamvu ndi oona ndi odzala ndi nthenthemya. Musukulu ya aphunzitsi anampeza Iye. Pamene anali nawonso, mayi Ake anati ndi mawu womulanga, "Mwana wanga wachitiranji ife chotero; taona atate Wako ndi ine tinalikukufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa." "Kuli bwanji kuti munali kundifunafuna Ine?," Yesu anayankha. "Kodi simunadziwa kuti kundiyenera Ine kugwira ntchito Yake ya Atate Wanga?" Pamene anaoneka kuti sanamvetsetse, Iye analoza kumwamba. Pankhope Pake panali kuwala umulungu. Unali kuwala kupyola mu umunthu. Iwo anamva za kukambirana kwa Iye ndi aphunzitsi ndipo anadabwitsika ndi mafunso ndi mayankho Ake. Apa Yesu anali otanganidwa ndi ntchito imene Iye anabwerera kudziko kudzaichita; koma Mariya ndi Yosefe yawo anainyalanyaza. Mulungu anawalemekeza iwo powapatsa mwana wake kuti asamalidwe ndi iwo. Koma kwa tsiku lonse iwo sanamuone Iye, pamene chikumbumtima chinawagwera, sanadziyese okha kulephera ntchito kwawo koma anamudzudzula Iye ngati analakwa ndi Iye. Mwachikhalidwe makolo a Yesu anamuona Iye ngati mwana wawo weniweni. Moyo Wake, mu zinthu zambiri, unali ofanana ndi ana ena ndipo kunali kobvuta kuti munthu adziwe kuti ndi Mwana wa Mulungu. Chidzudzulo chake chanzeru adachipanga kuwaonetsera makolo ake kufunika kwa ntchito imene Mulungu adamupatsa. Mu yankho Lake kwa mayi Ake, Yesu anaonetseratu poyera kwa nthawi yoyamba kuti amamvetsetsa ubale Wake kwa Mulungu. Mariya sanamvetsetse mawu Ake, koma anadziwa kuti Yesu anakana ubale ndi Yosefe ndikuti analengeza kukhala Mwana wa Mulungu. Kuchokera ku Yerusalemu, Yesu anabwerera kwawo ndi makolo Ake a pansi pano nawathandiza iwo m'ntchito zawo. Kwa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu Iye anadziwa ubale umene unam'mangirira Iye kunyumba ku Nazareti, nagwira ntchito ya mwana, m'bale, nzake ndi ya mbadwa. Chinali chifuniro cha Yesu kuti achoke ku Yerusalemu mwa kachetechete ndi iwo amene anadziwa chinsinsi cha moyo Wake. Pamwambo wa Pasika Mulungu amafuna kukumbutsa anthu Ake mu ntchito Yake yodabwitsa mu kupulumutsidwa kwawo kuchokera ku Iguputo. Mu ntchito Yake Iye amafuna iwo aone lonjezano la chipulumutso kuchokera kutchimo. Mwazi wa Yesu unayenera kupulumutsa mitima yawo. Mulungu anafuna kuti iwo atsogozedwe ku kupembedza poganizira ntchito ya Khristu. Koma khamu linachoka m'Yerusalemu, chikondwerero cha ulendo ndi kucheza amakopeka nazo kawirikawiri, ndipo mwambo umene amauona umaiwalika. Mpulumutsi sanakopeke kumagulu awo. Yesu Athandiza Mayi Wake K UCHOKERA KU Yerusalemu, Yesu anayembekezera kutsogolera Yosefe ndi Mariya ku maulauli a kuzunzika kwa Mpulumutsi. Pa Kalvale Iye anafuna kupeputsa chisoni cha mayi Ake. Anafuna kuwagonjetseratu nthawiyo isanakwane. Mariya anayenera kuona mazunzo Ake omaliza ndipo Yesu anafuna kuti amvetsetseretu cholinga chake, kuti adzathe kupirira pamene nthungo iti idzapyoze m'mtima wa mayi Ake. Ngati Mariya akanamvetsetsa Malembo amene Yesu anali kumutsogozera tsopano, bwenzi ululu wa imfa ya mwana wake utamupweteka pang'ono. Kunyozera kwa tsiku limodzi Yosefe ndi Mariya anataya Mpulumutsi; koma zinawatengera iwo masiku atatu kuti amfune namupeza Iye. Chimodzimodzinso ndi ife, kulankhula kopanda pake, kulankhula koipa, unyizi ndi pemphero, pa tsiku limodzi tingatayike m'manja mwa Mpulumutsi, ndipo izi zingatenge masiku ambiri kuti timpeze Iye ndikupezanso mtendere umene tautaya. Tiyenera kusamalira kuti tisaiwale Yesu ndi kuyenda mosaganiza kuti Iye sali ndi ife. Pokopeka ndi zinthu za m'dziko timadzilekanitsa tokha kwa Iye ndi kwa angelo akumwamba. Angelo oyerawa sangakhale kumene Mpulumutsi sakufunika ndi kusapezeka kwake nkosazindikirika. Ambiri amakhala pa misonkhano ya kupembedza, ndipo amatsitsimutsidwa ndi Mawu a Mulungu, koma kupyolera mu kunyozera ku kulingalira ndi pemphero, amataya madalitso. Podzipatula okha kuchokera kwa Yesu, adzitsekerezera okha kuwala Kwake kwa Mulungu. Kukadakhala kwabwino kwa ife kumakhala ndi ola limodzi tsiku ndi tsiku lomaphunzira za moyo wa Yesu. Tiyenera kutenga mutu ndi mutu ndi kutenga maganizo athu kuti agwire zochitika zilizonse, kwenikweni zomalizira. Ndiye chikhulupiriro chathu mwa Iye chidzakhala chosazima, chikondi chathu chidzatsitsimutsidwa, ndipo tidzadzazidwa ndi Mzimu Wake. Poona makhalidwe Ake abwino, "tidzasandulika mchithunzithunzi chomwechi kuchokera ku ulemerero kunka ku ulemerero." 2 Akorinto 3:18. |
Mutu 7 | Mutu 9 |