HOME
Mutu 8 Mutu 9 Mutu 10
Mabvuto a Umwana

N YAMATA ACHIYUDA amaphunzitsidwa ndi aphunzitsi amusunagogi potsatira malamulo osawerengeka amene amayembekezera kuti Aisrayeli awwasunge. Koma Yesu sanali okondweretsedwa mu zimenezi.
     Kuchokera mu umwana Iye sanakhale pansi pa arabbi ndipo sanasunge malamulo awo. Malembo anali maphunziro Ake, ndi mawu akuti, "Atero Ambuye," anali palilime Pake nthawi zonse.
     Iye anaona kuti anthu analikuchoka ku Mawu a Mulungu ndipo anali kusunga ndi kuphunzitsa miyambo yopanda ntchito. Mu chikhulupiriro chawo cha chabe sanapeze ntendere. Iwo sanadziwe ufulu wa uzimu umene umabwera pakutumikira Mulungu mu choonadi. Ngakhale Yesu sanabvomereze kusakaniza kwa miyambo ya anthu ndi chiphunzitso za Mulungu, sanatsutsane ndi zofuna ndi machitachita a aphunzitsi achiyudawa. Pamene anatsutsidwa chifukwa khalidwe Lake losadyerekezali, anapereka Uthenga wa Mulungu kufuna kuonetsa kusalakwa kwake pa makhalidwe ndi chitidwe Lake.
     Yesu anayesa kukondweretsa iwo amene anakomana nawo. Chifukwa Iye anali wa phee ndi wopanda makani, alembi ndi ansembe anayesa kuti Yesu akopeka ndi ziphunzitso zawo mosabvuta. Koma Iye anawafunsa ngati zochita zawo zinali zogwirizana ndi Malemba Oyera. Iye anamva mawu onse ochokera mkamwa mwa Mulungu, koma sangathe kumvera zopanga za anthu. Yesu anawaonetsera kudziwa malemba kuyambira pachiyambi mpaka ku mapeto ake ndikuwaphunzitsa monga mmene anayenera kuphunzitsidwa. Alembi analimbira kuti unali udindo wawo wofotokoza mawu a Mulungu ndi kuti Iye anayenera kutsata kumasulira kwawo.
     Iwo anadziwa kuti kunalibe ulamuliro mu malembo a miyambo yawo. Komabe iwo anakwiya chifukwa Yesu sanamvere ulamuliro wawo. Atalephera kuti amukope Iye, iwo anaitana Yosefe ndi Mariya ndi kumuneneza kuti Iye sanatsate malamulo awo. Choncho Iye anasautsidwa ndi ntonzo ndi nyozo.
     Ndi ku ubwana Kwake komwe Yesu anayamba kupanga makhalidwe Ake. Ngakhale chikondi cha pa makolo Ake sichikanatha kusintha kumvera Kwake pa Mawu a Mulungu. Koma chikoka cha alembi chinampweteka m'moyo Mwake. Anaphunzira phunziro lobvuta lodzikhazika chete osadzudzula ndi kupirira.
     Amene anali kutchedwa achimwene ake chifukwa anali ana a Yosefe, anali mbali ya alembi. Iwo anaona ngati miyambo ya wanthu inali yofunika kupambana mawu a Mulungu, namdzudzula Yesu kuti kunali kusamvera kumene kumampanga kuti adzingomvera malamulo a Mulungu okha basi. Podabwa ndi nzeru Zake m'mayankhidwe Ake kwa alembi, anadziwa kuti Iye anali mlangizi wawo. Anazindikira kuti maphunziro Ake anali a pamwamba osiyana ndi awo, komabe sanazindikire kuti Iye analikudziwa ndikugwiritsa ntchito gwero la nzeru zonse.

M'mene Yesu Analemekezera Anthu Onse Mofanana
K HRISTU ANAPEZA kuti chipembedzo chinazingidwa ndi makoma achitetezo ndi kuti chili chopatulika ndikuti munthu sangathe kukhala nacho m'moyo wake wa tsiku ndi tsiku. Iye anachotsa makomawa. M'malo modzipatula kukhala kupanga ndi cholinga chosonyeza khalidwe lakumwamba, Iye anatumikira anthu ndi mtima wonse. Iye anaphunzitsa kuti chipembedzo sichinali chongoonetsedwa pa nthawi yoikika kapena pamalo oikika. Ichi chinali chidzudzulo kwa Afarisi. Izi zinasonyeza kuti kudzipereka kwawo ku zinthu zimene amazikonda iwo kunawasendeza iwo kutali ndi choonadi cha Mulungu. Chidani chawo chinayamba, choncho iwo anakakamiza anthu kusunga miyambo ndi malamulo awo osati a Mulungu.
     Yesu anali ndi ndalama zochepa zopatsa osowa, koma Iye anadzikaniza yekha chakudya kuti akapatse iwo amene anali wosowa, ndi apansi, Yesu anayankhula kwa iwo mawu achilimbikitso. Kwa iwo amene anali osowa, Iye analikuwapatsa chikho cha madzi ozizira, ndi kuwapatsa m'manja mwawo, mwakachetechete, chakudya chimene anayenera kudya Iye.
     Zonse sizinakondweretse abale Ake. Monga akuluakulu Ake amakhulupirira kuti Iye ayenera kukhala mu ulamuliro wawo. Iwo amamuweruza Iye moganiza kuti amadziganizira yekha wopambana iwo onse, ndiponso amadzionetsera yekha ngati woposa aphunzitsi, ansembe, ndi wolamulira. Kawirikawiri iwo amayesetsa kuti amuopsyeze Iye, koma Iye amapitirira, ndi kupanga malembo monga chitsogozo Chake.

Mabvuto a Yesu mu Banja Lawo
A BALE AKE a Yesu anamchitira Iye nsanje ndipo anamuonetsera chikaiko ndi chidani. Iwo sanamvetsetse zochita Zake. Panali kusiyana kwakukulu pakati pa moyo Wake ndi wa abale Ake. Iye anali Mwana Wopatulika wa Mulungu, komabe anali mwana wopanda chithandizo. Ngakhale Iye anali Mlengi, ndikuti dziko lonse lapansi linali Lake, umphawi unaonekera m'moyo Wake. Iye sanalimbire ukulu wa dziko, ndipo anakwanitsidwa ndi malo a munthu wamba. Izi zinakwiyitsa abale Ake. Iwo sanathe kumvetsetsa mmene Iye analikuthera kukhala wofatsa m'mayesero ndi m'kusowa.
     Abale Ake sanamumvetsetse Yesu chifukwa anali wosiyana ndi iwo. Potsanzira za wanthu, iwo anafulatira Mulungu ndipo analibe mphamvu Zake m'miyoyo yawo. Chipembedzo chimene anachitsata sichikanatha kusintha makhalidwe awo. Chitsanzo cha Yesu kwa iwo chinali kuwabvutitsa nthawi zonse. Iye amadana ndi tchimo ndipo nthawi zonse akaona choipa chikupangidwa amaonetsa kuwawidwa mtima kosamveka. Chifukwa moyo wa Yesu unadana ndi zoipa, Iye anatsutsidwa. Kupanda dyera Kwake ndi kuona mtima Kwake zinapangitsa abale Ake kumunyoza Iye. Kupitirira ndi kukoma mtima Kwake anazitembenuza kuti amaonetsa kuti ndimunthu wamantha.
     Zowawitsa za moyo zimene zimagwera wanthu, zonse Yesu zinamugwera. Panalibe mbali imene Khristu sanayesedwe. Ena anadana naye chifukwa cha kubadwa Kwake. Ngakhale mu ubwana Wake anakomana ndi wonyoza ndi amiseche opanda pake. Ngati Iye akadabwezera ndi mawu asontho kapena kuyang'na koipa kapena choipa chimodzi, Iye adakalephera kukhala chitsanzo chabwino. Kotero kuti Iye akadalephera kukonza chilinganizo cha chipulumutso chathu. Iye akadangobvomereza kuti kuchimwa kulikonse kuli ndi chifukwa chake, Satana akadagonjetsa, ndipo dziko likanakhala lotayika. Kawirikawiri anamuona ngati wamantha pokana kugwirizana ndi abale Ake mu zinthu zoipa, koma kuyankha Kwake kunali kwa kuti, Kwalembedwa, "Kuopa Ambuye ndi nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha." Yobu 28:28.
     Ena anapeza ufulu mwa Iye, koma ambiri anampewa Iye natsutsika ndi moyo wake wopanda banga. Achinyamata amzake anasangalala naye, koma anali kukhumudwa ndi kutsutsidwa kwawo poyerekeza miyoyo yawo ndi moyo wa Yesu wachilungamo, namutcha Iye wakumva zake zokha ndi wotsalira. Yesu anayankha, Kwalembedwa, "Kodi mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Adawasamalira monga mwa mawu Anu. Ndinawabisa mawu Anu mu mtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu." Masalimo 119:9,11.
     Kawirikawiri anafunsidwa, Bwanji umangolimbikira kukhala wosiyana ndi ife? Kwalembedwa, Iye ananena, "Odala iwo akusunga mboni zake, iwo amene salakwa, koma amayenda m'njira Zake!" Masalimo 119:2,3.
     Yesu sanamenyere ufulu wa makhalidwe Ake. Iye sanabwezere choipa, koma m'kunyozedwa konse anapirira mofatsa. Nthawi ndi nthawi anali kufunsidwa, Bwanji umalolera kunyozedwa, ngakhale ndi abale Ako omwe? Ananena, Kwalembedwa "Mwana wanga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga...chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; motere udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu." Miyambo 3:1-4.

Chifukwa Chimene Iye anayenera kukhala Osiyana ndi Ena
M ACHITIDWE a Yesu anali odabwitsa kwa makolo Ake. Anaoneka kuti anali munthu wopatulidwira kuntchito yina. Maola achisangalalo Chake amapezeka pokhala pa Yekha ndi chilengedwe ndi Mulungu. Kawirikawiri kukamacha amapezeka pamalo apa Yekha, kusinkhasinkha, kusanthula malembo kapena mu pemphero. Akatha maola achetewa anali kubwerera ku mudzi kukagwira zintchito Zake.
     Mariya anakhulupirira kuti mwana wangwiro anabadwa mwa iye anali Mesiya, koma sanasonyeze chikhulupiriro chake. Moyo Wake wonse anatenga naye mbali mu zobvuta Zake. Mwachisoni anachitira umboni mayesero amene anamudzera Iye mu umwana ndi unyamata Wake. Pakumuimira mwana wake mumakhalidwe amene anthu ena samatha kumumvetsetsa Mariya anayesedwa munjira zambiri. Iye anazindikira kuti chikoka cha mayi pawana m'banja nchofunika kwambiri chifukwa chimawathangata ana kupanga khalidwe. Ana amuna ndi akazi a Yosefe anadziwa izi ndipo amayesetsa kupyolera m'chikoka cha mayi a Yesu, kugwedza ndi kupotoza machitidwe a Yesu malingana ndi mbendera za chikhalidwe chawo.
     Kawirikawiri Mariya anali kuyesetsa kumuuza Yesu kuti azigwirizana ndi aphunzitsi. Koma Iye sanathe kuumirizidwa kuti asinthe makhalidwe Ake oganizira ntchito za Mulungu ndi kuchepetsa mabvuto awanthu. Pamene ansembe ndi aphunzitsi amafuna chithandizo cha mayi Ake kuti amulamulire Yesu, iye anabvutidwa kwambiri; koma mtendere unabwera mu mtima mwake pamene Yesu anaonetsera kuchokera mu zolembera...chifukwa chimene anali kuchitira ntchito Yake.
     Nthawi zina Mariya amalowa m'gulu la abale Ake a Yesu omwe sanali kumukhulupirira kuti Iye anali Wotumidwa ndi Mulungu, koma panali umboni wochuluka kuti Iye anali nalo khalidwe la Umulungu. Moyo Wake unali ngati chotupitsa chogwira ntchito mkati mwa amitundu. Mosadetsedwa, Iye anayenda pakati pa anthu osaganiza bwino, amwano, opanda khalidwe, pakati pa akunja opanda chilungamo, adyera, ndi Asamariya ochimwa, asilikali achikunja, anthu wamba ndi amitundu osiyanasiyana. Iye analankhula mawu achifundo pamene anaona anthu otopa akuumirizidwa kusenza katundu wolemetsa. Iye anabwereza kuwaphunzitsa ziphunzitso zimene anaziphunzira kuchokera ku chilengedwe cha chikondi ndi ubwino wa Mulungu.
     Iye anawaphunzitsa iwo kuti azidziyang'ana monga odalitsika ndi matalente wopambana. Kupyolera Mnzitsanzo, Iye anaphunzitsa kuti mphindi iliyonse iyenera kuonedwa ngati chuma ndi kugwiritsidwa mu ntchito zopatulika. Iye sanadutse munthu wina aliyense ngati opanda ntchito, koma anafuna kuwauzirira ndi chiyembekezo obvutawo ndi opanda chiyembekezowo, kuwatsimikizira iwo kuti angathe kukhala ndi khalidwe labwino limene lingawapange iwo kuonetsera kwa anthu kuti ndi ana Ake a Mulungu. Kawirikawiri Iye anakomana ndi iwo amene analibe mphamvu zotha kudzimasula kunsinga za Satana. Kwa otere, ogwetsedwa mphwayi, odwala, am'mayesero ndi akugwa, Yesu ankalankhula mawu achilimbikitso ndi achitonthozo.
     Wena amene anakomana nawo analikumenyana nkhondo yeniyeni ndi mdani wa miyoyo. Iwowa anawalimbikitsa kuti apirire chifukwa angelo a Mulungu anali pambali pawo ndikuti akanawapatsa iwo chigonjetso. Iwo amene Iye anawathandiza anakhutitsidwa kuti tsopano anapeza m'modzi amene iwo anayenera kumkhulupirira ndi chikhulupiriro changwiro.
     Yesu anaonetsera chidwi ndi mbali iliyonse ya msautso, ndipo kwa osautsidwa aliyense Iye anapereka chitonthozo, mawu Ake okoma anali ngati mankhwala. Palibe amene angati Iye anali kuchitira matsenga, koma Umulungu?mphamvu ya chiza yo chikondi?zinachoka mwa Iye. Ndiye mosaumirizidwa Iye anagwirira ntchito kuyambira ubwana Wake.

Mutu 8 Mutu 10