HOME
Mutu 9 Mutu 10 Mutu 11
Mawu a M'chipululu

K UCHOKERA PAKATI PA OKHULUPIRIRA mu Israeli obwera patsogolo pa Khristu anauka. Zakariya wansembe wokalambayo ndi mkazi wake Elizabeti "anali wolungama pamaso pa Mulungu." Ndipo m'mimoyo yawo yaphee kuunika kwa chikhulupiriro kunawala ngati nyenyezi mu mdima. Kwa iwo kunapatsidwa lonjezano la mwana wa mwamuna amene "ati adzapite patsogolo kukonza makhwalala a Ambuye."
     Zakariya anapita ku Yerusalemu kukagwira ntchito za unsembe m'kachisi kwa Sabata imodzi. Atayima pa guwa la nsembe m'malo opatulika, mwadzidzi iye anaona mngelo wa Ambuye "ataima chakumanja kwa guwa." Kwa zaka zambiri anali kupempherera kubwera kwa Mpulumutsi; tsopano mapemphero amenewa anali pafupi kuyankhidwa.
     Analonjezedwa ndi chisangalalo chotsimikizika: "Usaope Zakariya: pemphero lako lamveka; mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wa mwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane...Adzakhala wamkulu pa maso pa Ambuye, ndipo sadzamwa vinyo kapena chakumwa chili chonse choledzeretsa; adzadzazidwa ndi Mzimu Woyera...Adzapita patsogolo pa iye mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kubwezera mitima ya abeleki kwa wana ndi osamvera kunzeru ya olungama, kukonzetsera anthu kubwera kwa Ambuye.' Zakariya anati kwa mngelo, `Ndidzadziwa bwanji? Pakuti ndine wokalamba ndi mkazi wanganso.'"
     Mwa kanthawi wansembe wachikulireyu anaiwala kuti chimene Mulungu walonjeza chimenecho adzachichita. Taonani kusiyana pakati pa kusakhululpirira kwake ndi chikhululpiriro cha Mariya, pamene yankho kwa mngelo linali la kuti, "Taonani, ndine mkazi wa Ambuye; chichitike kwa ine monga kwa mawu anu." Luka 1:38.
     Kubadwa kwa mwana wa mwamuna wa Zakariya, monga kubadwa kwa mwana wa Abrahamu, ndi uja wa Mariya, kunali kuphunzitsa choonadi chachikulu: Icho chimene sitingathe kuchichita chidzachitika ndi mphamvu ya Mulungu m'moyo uli wonse wokhulupirira. Mwa chikhulupiriro mwana wa lonjezano anapatsidwa. Mwa chikhulupirironso moyo wachikhristu umabadwa, ndipo timayeneretsedwa kuchita ntchito zachilungamo.
     Zaka mazana asanu isanafike nthawiyi Mngelo Gabriyele anamuzindikiritsa Danieli za ulauli wa nthawi imene inadzathera pakubadwa kwa Khristu. Nzeru zakuti nthawi imeneyi inali pafupi inampangitsa Zakariya kupempherera za kubwera kwa Mesiya. Tsopano, mngelo yemweyo amene anadzapereka ulosi umenewu anabweranso kudzanena za kukwaniritsidwa kwake.

Zakariya Anakayikira
Z AKARIYA ANAONETSERA CHIKAIKO pa mawu a mngelo. Ndipo anauzidwa kuti salankhulanso kufikira zitakwanitsidwa, "Tanonani udzakhala chete, osatha kulankhula kufikira tsiku lodzachitika zimenezi, chifukwa sunakhulupirire mawu angawa amene adzachitikadi panthawi yake." Inali ntchito ya ansembe pa utumikiwu kupempherera chikhululukiro cha machimo ndi kubwera kwa Mesiya; Zakariya anayesa kupanga ichi koma sanathe kulankhula. Pamene anatuluka mu kachisi nkhope yake inawala ndi ulemerero wa Mulungu ndipo anthu "anazindikira kuti anaona masomphenya m'kachisi." Zakariya "anakhala osalankhula" koma kupyolera mu "zisonyezo" anawadziwitsa anzake pa zimene anaona ndi kumva.
     Atangobadwa mwana wa lonjezano lilime la bambo wake linamasuka. "Ndipo nkhani iyi inali mkamwa mwa wanthu dziko lonse la Yudeya; onse amene anamva anadzifunsa okha m'mitima yawo nati 'mwanayu adzakhala wotani?'" Zonsezi zinawatsimikizira zakubwera kwa Mesiya. Mzimu Woyera unatera pa Zakariya ndipo analosera za ntchito ya mwana wake.
Mwana iwe udzatchedwa mneneri wa Mulungu wakumwambamwamba, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zawo. Udzadziwitsa anthu awo kuti Mulungu afuna kuwapulumutsa Ndi kukhululukira machimo awo.
     "Mwanayo anakula ndi luntha la mphamvu mu uzimu, ndipo anali m'chipululu kufikira tsiku limene anadzionetsera yekha kwa Israyeli." Mulungu anaitanira mwana wa Zakariya ku ntchito yopambana imene ndikale lonse siinapatsidwe kwa wina aliyense. Ndipo Mzimu wa Mulungu udzakhala naye ngati amvera ndi kuchita monga mwa malangizo a mngelo.
     Yohane anayenera kubweretsa kwa wanthu kuunika kwa Mulungu. Ayyenera kuwatsimikizikira iwo zokhumba zawo za ungwiro Wake. Mtumiki wotere ayenera kukhala woyera, kachisi wokhalamo Mzimu Woyera wa Mulungu. Ayenera kukhala ndi thupi loumbidwa bwino, ndi mphamvu za maganizo ndi za uzimu. Choncho zinali zoyenera kuti akhale wodziletsa ku zilakolako zonse za thupi.
     Munthawi ya Yohane Mbatizi, dyera la chuma ndi kukonda mtambasale ndi kudzionetsera zinachuluka. Zokondweretsa za dama, kudya ndi kumwa, zinali kufooketsa thanzi la wanthu, ndi kuchepetsa mphamvu ya uzimu kuti sanathe kuzindikira ndikuukana uchimo. Yohane anayenera monga wokonzanso. Ndi moyo wake wodziletsa ndi mabvalidwe olongosoka anayenera kudzudzula anthu a mu nthawi yake. Ndicho chifukwa chake phunziro lakudziletsa linaperekedwa ndi mngelo kwa makolo ake kuchokera ku mpando wachifumu wa Kumwamba.
     Mu ubwana ndi mu unyamata mphamvu yodzilamulira iyenera ku kulitsidwa. Zizolowezi zokhazikitsidwa mu zaka zoyambirira zidzaonetsera ngati munthu adzakhala wogonjetsa kapena wogonjetsedwa mu nkhondo ya moyo. Unyamata, nthawi ya kufesa, imatsimikizira khalidwe la kholola, m'moyo uno ndi m'moyo ulinkudza.
     Pokonzetsera njira ya kudza koyamba kwa Khristu, Yohane anali oyimirira wa anthu awo okonzekera kudza kachiwiri kwa Ambuye. Dziko ladzipereka ku kusadziletsa kuphunzira. Zisokonekero ndi mabodza zili ponse ponse. Onse amene akufuna kukhala angwiro mukuopa Mulungu ayenera kudziletsa ndi kudzilamulira. Onani 2 Akorinto 7:1. Zilakolako ndi umunthu ziyenera kulamulidwa ndi mphamvu ya maganizo. Kudzichongaku nkofunika kuti munthu ukhale ndi maganizo amphamvu ndi mphamvu ya uzimu imene imatipangitsa ife kumvetsetsa ndi kuchita nacho choonadi cha mawu a Mulungu.

Maphunziro Odabwitsa A Yohane
N DI MOMWE ZINTHU zinaliri, mwana wa Zakaria akadayenera kukaphunzira mu sukulu za wana aneneri. Komabe izi sizidakayenerana ndi ntchito yomwe Mulungu adamuyitanira, choncho Mulungu adamuitanira ku chipululu kuti akaphunzire za zolengedwa ndi Mulungu wachilingedwe.
     Yohane anadzipezera malo okhala kumapiri opanda kanthu, kumaphompho ndi kumapanga. Kumeneku zonse zomuzungulira zinali zomuthangata kupanga makhalidwe wodzichepetsa ndi wodziletsa. Ukunso akana kuphunzira za zolengedwa, chibvumbulutso, ndi chipatso. Mu ubwana wake makolo ake oopa Mulunguwo ankankumbutsa za ntchito yake ndipo iye analandira ntchito yopatulikayo. Pokhala iye m'chipululu kwayekha adadzilekanitsa yekha ndi gulu la anthu limene kwathunthu ndi wanthu mtundu wake linadzaza kusakhulupirira ndi zonyasa zopanda malekezero. Iye anadziletsa kuti asayandikirane kapena kuzolowerana ndi uchimo, kuti angafike pamalo osaona kunyansa kwake kwa tchimo.
     Yohane sanakule m'moyo wochita zofuna zake ndi wodzipatura. Nthawi ndi nthawi anali kusakanikirana ndi wanthu, nakhalanso wokondweretsedwa kupeza zomwe zinali kuchitika m'dziko. Potsogozedwa ndi mphamvu ya Mzimu woyera anaphunzira njira zimene anakathera kufikira mitima ya wanthu ndi uthenga wa Kumwamba. Katundu wa chintchito chonsechi anali pa iye. Kupyolera m'kusinkhasinkha ndi mapemphero iye adaukonzetsera moyo wake ku chintchito chimene chinali patsogolo pake.
     Ngakhale anali m'chipululu iyenso anali kuyesedwa. Anayesedwa ndi wonyengayo koma maganizo ake anzimu anamuchinjiriza ndipo kupyolero mwa Mzimu Woyera anakhoza kumudziwa ndi kukana mayesero a Satana kuwazindikira ndi kuwapewa.
     Monga Mose pakati pamapiri a ku Midiani, Yohanenso anafungatiridwa ndi Mulungu. Masautso ndi kubvuta kwa zinthu m'chipululumo zidamuonetsera bwinobwino momwe Israyeli analiri. Munda wa mpesa wa Ambuye unapangidwa kukhala bwinja. Koma mumlengalenga, mitambo yakuda yamvula inalengedwa ndi utawaleza wa chipangano, kuonetsa kuti kaya zibvute maka chigonjetso sichidzalephereka.
     Yekha muusiku wachete anali kuwerenga za pangano la Mulungu kwa Abrahamu monga mtundu osawerengeka ngati nyenyezi. Kuwala kwa mabingakucha kunamudziwitsa za iye amene adzakhale ngati "kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, m'mawa wopanda mitambo." 2 Samueli 23:4. Ndipo m'kuwala kwa masana anaona kunyezima pamene "ulemerero wa Yehova uti udzabvumbulitsidwe, wanthu onse nadzamuona pamodzi." Yesaya 40:5.
     Mwa mantha komanso mwa mzimu wa chisangalalo, anafufuza m'mipukutu ya ulauli yowonetsera za kudza kwa Mesiya. Shilo adayenera kukaonana ndi mfumu asadasiye kulamulira mu ufumu wa Davide. Tsopano nthawi inafika. Olamulira wachiroma anali m'nyumba ya chifumu pa phiri la Zioni. Mwa choonadi cha mawu a Ambuye, Khristu nkuti atabadwa kale.

Zolembera za Yesaya Zisanthulidwa
U SANA NDI USIKU iye anali kuphunzira za ulemerero wa Mesiya kupyolera mu zolembera za Yesaya. Onani Yesaya 11:4; 32:2; 62:4. Mtima wa wamundende m'chipululu unadzaza ndi masomphenya a ulemerero. Anaona Mfumu m'kukongola Kwake ndipo undekha unayiwalika. Anayang'anitsitsa Karonga wopatulikayo, nadziona kuti anali wolephera ndi wosayenera. Anali okonzeka kupita chitsogolo monga mtumiki wa mwambamwamba, opanda mantha ndi wanthu kamba kakuti anapenyetsetsa oyerayo. Ndipo ankatha kuyima pamaso pa olamulira pansipano opanda mantha chifukwa chodzichepetsa pamaso pa Mfumu ya mafumu.
     Yohane sanamvetsetse za makhalidwe a ufumu wa Mesiya, komanso za kubwera kwa mfumu ya chilungamoyo ndi kukhazikitsidwa kwa Israyeli monga mtundu wopatulika, chinali chinthu chopambana chomwe anakachiyembekezera. Anaona anthu ake ali okwanitsidwa ndiponso ali m'tulo mu machimo awo. Uthenga umene Mulungu anamupatsa iye unali owadzutsa iwo kuchokera kutulo tawo. Mbewu ya uthenga isanapeze malo, dothi la m'mtima liyenera kuphwanyidwa ndikukonzedwa. Asanafune machilitso kuchokera kwa Yesu, ayenera adzutsidwe kuti aone ndikuzindikira kuopsya kwake kwa mabala a uchimo.
     Mulungu satumiza amithenga ake kukasusuza mpakana kukawagoneka osasankhika muchitetezo chabodza. Iye amayika goli lolemera pa chikumbumtima cha wolakwa nalasa moyo ndi mivi ya chidzudzulo. Angelo otumikira amapereka ziweruzo zoopsya za Mulungu pofuna kukhwimitsa maganizo ofunika. Ndipo dzanja lodzichepetsa mufumbi limanyamula odzipereka.

Kumayambiriro a Nthawi ya Kukonzanso
P AMENE UTUMIKI WA YOHANE unayamba, nkuti dziko litatsala pang'ono kuti likonzenso boma. Pochotsedwa Akelayo, Yudeya anatengedwa nakhala pansi pa ulamuliro wa a Roma. Kuzunza ndi kulamulira kwa nkhanya kwa olamulira Achiroma ndi kufuna kubweretsa makhalidwe ndi ziphunzitso za chikunja, kunayatsa chipolowe chimene chinazimitsidwa m'magazi a wanthu miyandamiyanda olimba mtima Achiisraeli.
     Pakati pa mikangano ndi nkhwidzi mawu anamveka m'chipululu, odabwitsa, ozikizira mchikumbu mtima ndi achilendo koma achiyembekezo chodzaza; "Tembenukani mtima pakuti ufumu wakumwamba wayandikira," ndi mphamvu yachilendo yatsopano anthu anatekeseka. Uku kunali kulengeza kwakuti kubwera kwa Khristu kunali pafupi. Mu muzimu ndi mphamvu ya Eliya, Yohane anatsutsa kuipa kwa dziko ndi kudzudzula uchimo unkachitika. Mawu ake anali olasa ndi ogwira moyo. Dziko linagwedezeka. Miyandamiyanda ya anthu inathamangira ku chipululu.
     Yohane anawaitanira wanthu kukolapa. Monga chionetsero choyeretsa munthu uchimo, anawabatiza iwo m'madzi a mtsinje wa Yordano. Choncho anaonetsera kuti onse amene anadzitcha anthu osankhika a Mulungu anali a uchimo. Kopanda kudziyeretsa kwa mtima sakanakhala ndi mbali mu ufumu wa Mesiya.
     Akalonga, Alembi, asilikali a nkhondo a msonkho ndi anthu wamba anabwera kuzamvera m'neneri. Ambiri anatembenuka mitima nalandira ubatizo kuti atenge mbali muufumu unkalengezedwawo.
     Alembi ndi Afarisi ambiri anabwera kudzalapa machimo awo ndi kufuna kuti abatizidwe. Anawatsogolera anthu kumaganizo akuti Afarisi ndi Alembiwo anali wolungama kwambiri koma tsopano chikumbumtima chakulakwa kwa miyoyo yawo yamseli chinaonekera. Yohane anadabwitsika kuti anthu ambiri a amenewa sanali kugonja ku uchimo. Anali anthu ongotembenuka chifukwa cha nthawi. Monga abwenzi a mneneri ankayembekezera kuti adzapeze malo pamwamba ndi chikondwerero mu ufumu unali nkudza. Ndipo polandira ubatizo amaganiza kuti akulimbikitsa chikoka chawo pa anthu.

Kudzudzula kwa Yohane kwa Onyenga
Y OHANE ANAWADZUDZULA ndi mphamvu, "Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza? Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima." Ayuda anadzichotsa okha kwa Mulungu, ndi chifukwa chake anali kubvutika ndi chiweruzo chake. Ndiye chifukwa chake anakawalowetsa mu ukapolo. Popeza mbuyomo Mulungu anawaonetsera kulekelera kwa kukulu, ndicho chifukwa chimene iwo sanalabadire uchimo wawo. Anadzinyenga okha kuti anali bwino koposa anthu wena ndikuti madalitso a Mulungu anali awo.
     Yohane anawaonetsera poyera aphunzitsi a mu Israeli kuti kudzikonda kwawo, dyera lawo, ndi nkhanza zawo zinaonetsera kuti anali tembelero kwa wanthu. Pakuona kuunika kumene analandira kwa Mulungu kuipa kwawo kunaposa anthu achikunja. Mulungu sanali kudalira pa iwo kuti akukwaniritse zofuna zake. Akanitana wena ku ntchito yake.
     "Tsopano," mineneri anati, "nkhwangwa yaikidwa pa tsinde la mtengo, uli wonse umene subereka zipatso zabwino umagwetsedwa, ndi kuotchedwa." Ngati chipatso chili chachabe, dzina chabe silingapulumutse mtengo kuti usaonongedwe. Yohane ananeneratu poyera kwa ayuda kuti ngati moyo wawo ndi khalidwe lawo silinali kufanana ndi malamulo a Mulungu, sanali wanthu ake.
     Onse amene akufuna kukhala nzika za ufumu wa Khristu ayenera kupereka umboni wa chikhulupiriro ndi kulapa kotheratu. Chifundo ndi chiyero ziyenera kuwonekere mu miyoyo yawo. Ayenera atumikire osauka, atchinge opanda mphamvu, napereka chitsanzo cha chilungamo ndi chisoni.
<     "Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto." Yesaya ananena kuti Ambuye adzayeretsa anthu Ake. "Ndi mzimu wa chiweruzo, ndi mzimu wakuyaka." Yesaya 4:4.
     Kwa onse amene agonjera ku mphamvu yake Mzimu wa Mulungu udzathetsa tchimo. Onani, Ahebri 12:29. Koma ngati anthu aumilira ku uchimo, ulemerero wa Mulungu umene umaononga uchimo, uononga iwo. Pakubwera kwachiwiri kwa Khristu ochimwa adzaphedwa ndi "mzimu ochokera mu mkamwa mwake," ndi kuonongeka ndi kunyezimira kwa kubwera kwake. 2 Atesolonika 2:8. Ulemerero wa Mulungu umene umapereka moyo kwa olungama udzapha ochimwa.
     Munthawi ya Yohane mbatizi, Khristu anali pafupi kuoneka ngati obvumbulutsa khalidwe la Mulungu. Kubwera kwake kunaonetsera kwa anthu zochimwa zawo. Pokhapo anali olola kusiya zolakwa zawo ndi pamene anali pa ubwenzi ndi Iye.
     Ndi m'mene m'batizi anaonetsera uthenga wa Mulungu kwa Israeli. Ambiri anamvera ndipo anapereka nsembe zonse kuti amvere. Ambiri anakhulupirira kuti ayenera kukhala Mesiya. Koma pamene Yohane anaona anthu akubwera kwa iye, anasakasaka njira iliyonse yowatsogolera chikhulupiriro chawo kwa Iye amene anali kubwera.

Mutu 9 Mutu 11