HOME |
Mutu 10 | Mutu 11 | Mutu 12 |
U THENGA WA MNENERI wa mnkhalango unawafika anthu wamba okhala m'mapiri a mtalimtali ndi asodzi a nsomba amene amakhala kunyanja ndipo m'mitima iyi yodzichepetsa yachidwi unalandiridwa ndi kukhazikika. Mu Nazareti uthengawu unamveka mu nyumba yopalira matabwa ya Yosefe, ndipo M'modzi anazindikira kuitanako. Nthawi Yake inafika. Anatsazika mayi Ake natsata anthu a m'mudzi amene amapita ku Yordani. Yesu ndi Yohani anali pachisuwani, koma sanali kudziwana kwenikweni. Mulungu adazikonza kuti zikhale choncho. Mulungu anachita izi kuti wina asadzati awiriwa adachita kupangana kuti ampange Yesu kukhala mwana wa Mulungu. Yohane anazolowerana ndi zinthu zochitika zimene zinasonyeza kubadwa kwa Yesu, Iye anamva za kucheza kwa Yesu ku Yerusalemu mu unyamata Wake, ndi moyo umene anakhala opanda tchimo. Iye anakhulupirira kuti Yesu anali Mesiya, koma popeza Yesu adadzibisa, osafuna kuonetsera ntchito imene anadza kudzachita. Zidampangitsa Yohane kumukaikira Yesu. Yohane mbatizi anayembekezera m'chikhulupiriro. Zidaonetsedweratu kwa Yohane kuti Mesiya adzamfunsa kuti amubatize, ndikuti chizindikiro cha khalidwe Lake la umulungu likaonetsedwe kwa anthu. Pamene Yesu anadza kudzabatizidwa, Yohane amzindikira mwa Iye khalidwe langwiro limene m'khale lonse silinaonetsedwe ndi munthu. Kuonekera Kwake kunali koonetsa ulemu. Izi zinali kugwirizana ndi zimene zinaululidwa kwa Yohane ponena za Mesiya. Koma zidakatheka bwanji kuti iye wochimwa kubatiza wosachimwayo? Kodi nchifukwa chiyani Iye amene samafunika kulapa anadzipereka ku mchitidwe wa kupereka machimo kuti atsukidwe? Yesu atafunsa zoti abatizidwe, Yohane anati amkanize, nanena "'Ndiyenera ine kuti ndibatizidwe ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?' Koma Yesu anayankha nati kwa iye, 'Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motere.' Pamenepo iye analola. Ndipo pamene Yesu anabatizidwa anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inatsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye." Yesu Wosachimwa Abatizidwa Y ESU SANALANDIRE UBATIZO monga kulapa kwa machimo a Iye mwini. Anakhala pamodzi ndi ochimwa nayenda monga mmene ife tikuyendera ndikuchita monga mmene timachitira ndi moyo. Atabatizidwa, moyo Wake wobvutika ndi wopirira unalinso chitsanzo kwa ife. Atatuluka m'madzi, Yesu anawerama napemphera m'mbali mwa mtsinje. Iye anali kulowa chimkangano chachikulu cha moyo Wake. Ngakhale anali Kalonga wa Mtendere, kubwera Kwake kunali ngati kutulutsidwa kwa lupanga mchimake. Ufumu umene Iye anabwerera kudzakhazikitsa unali wotsutsana ndi umene Ayuda amafuna. Iye akadaonedwa ngati mdani ndi woononga mwambo ndi chipembedzo cha chiisraeli, natsutsidwa monga woswa lamulo ndikunyozedwa ngati Belezebabu. Panalibe ndi m'modzi yemwe padziko lapansi amene adamvetsetsa, ndipo anayeneradi kuyenda yekha. Mayi ndi abale Ake sanamvetsetse cholinga Chake. Ngakhale ophunzira Ake sanathe kummvetsetsa. Monga m'modzi wa ife, ayenera kubvala uchimo ndi mabvuto a anthu. Munthu wosachimwayo ayenera kumvera manyazi a tchimo. Wokonda mtendereyo ayenera kukhala pamodzi ndi mkangano, choonadi chiynera kukhala ndi chabodza, choyera chiyenera kukhala ndi choipa. Tchimo lililonse, mkangano uliwonse, ndi chisiliro chonse chonyansa chinali chipsyinjo kwa m'mzimu Wake. Yekhayekha ayenera kuyenda m'njirayi. Pa Iye amene analandira zofooka za amitundu, mwa Iye chiombolo cha dziko lapansi chiyenera kukhazikitsidwa. Anaona ndi kumva bwinobwino, koma cholinga Chake sichinasinthike. Mpulumutsi anakhuthula mzimu Wake mu pemphero. Anadziwa mmene tchimo linaumitsira mitima ya anthu, ndi mmene zikanabvutira kuti anthu amvetsetse uthenga Wake ndikulandira chipulumutso. Iye anapembedzera kwa Atate kuti ampatse mphamvu zoti agonjetsere kusakhulupirira kwawo, kudula zingwe zomwe Satana anawamangira iwo, ndi kugonjetsa wowonongayo. Ndikale lonse angelo anali asanamvepo pemphero lotero. Atate mwini Wake yekha ndiye amene akanatha kuyankha pempho la Mwana Wake. Miyamba inatseguka, ndipo kuyera kwakukulu konga nkhunda kunatera pa mutu wa Mpulumutsi. Ambiri kupatula Yohane pa Yordano anadabwitsika ndipo sanamvetsetse zooneka zakumwambazi. Koma chikoka cha ulemerero wa Mulungu chinakhala pa iwo onse. Nkhope ya Yesu yomwe inayang'ana kumwamba inawala ndi ulemerero woti sanaonenso chochitika chotere pa nkhope ya munthu wina aliyense wa padziko lapansi. Kuchokera kumwamba kotsekukako mawu anamveka "Uyu ndiye Mwana Wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera naye." M'mwamba Muchitira Umboni M AWU AWA analankhulidwa kuti alimbikitse chikhulupiriro mwa iwo amene anaona zochitikazo ndi kulimbikitsanso Mpulumutsi pa ntchito Yake. Posapeputsa lakuti machimo a dziko loipali anaikidwa pa Khristu, posapeputsa ganizo lakuti anadzichepetsa pakutenga khalidwe ndi maonekedwe a anthu akugwa, mawu ochokera kumwamba analengeza kuti iye adzakhala mwana wa muyaya. Yohane anakhudzidwa kwambiri. Pamene ulemerero wa Mulungu unamkuta Yesu ndi mawu ochoka kumwamba anamveka, Yohone anadziwa kuti anali Mombolo wa dziko lapansi amene iye anambatiza. Ndi dzanja lotambasuka akuloza Yesu, napfuula "Toanani, mwana wa nkhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi." Yohane 1:29. Mwa omvetserawo, ngakhale wolankhula amene sanathe kuzindikira kufunika kwa mawuwa, "Mwana wa nkhosa wa Mulungu." Anthu ambiri a m'Israeli amakhulupirira kwambiri mu msembe za zopereka monganso mmene achikunja amakhulupirira mu msembe zawo Mphatso zopanga chigwirizano ndi Mulungu. Mulungu anafuna kuwaphunzitsa kuti kuchokera mu chikondi Chake ndi mmene mwatuluka Mphatso yolumikiza iwo kwa Iye mwini. Uyu ndi Mwana Wanga L iwu lolankhulidwa kwa Yesu, "Uyu ndi mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera," lafungatira mtunda wa anthu. Ndi machimo athu onse ndi kufooka kwathu konse sitinataidwe kunja monga anthu opanda ntchito. "Watipanga ife kuti tilandiridwe mwa wokondedwayo." Aefeso 1:6. Ulemerero umene unakhala pa Khristu ndi lumbiro la chikondi cha Mulungu pa ife. Umatiuza ife za mphamvu ya pemphero limene mawu athu amafikira mkhutu la Mulungu, ndi mmene mapemphero athu amalandiridwira ku mabwalo a Kumwamba. Kupyolera mu tchimo, dziko lapansi linalekanitsidwa ndi la Kumwamba, koma Yesu walilumikizanso ndi ulemerero Wake. Kuwala komwe kunagwa pa mutu wa Mpulumutsi wathu kudzagwanso pa ife pamene tipempha mphamvu zotitchinjiriza ku mayesero. Mawu amene analankhulidwa; kwa Yesu akunenedwabe kwa yense wokhulupirira, Uyu ndiye mwana Wanga wokondedwa mwa iyeyu ndikondwera. Mombolo wathu watsegula njira kuti munthu wochimwitsitsa, wopsyinjika ndi wonyozedwa akapeze mwayi wofika kwa Atate. Onse akapeze nyumba mu mzinda umene Yesu anapita kukatikonzera. |
Mutu 10 | Mutu 12 |